Yoswa 18 BL92

Autsa cihema ku Silo

1 Ndipo msonkhano wonse wa ana a Israyeli unasonkhana ku Silo, nuutsa komweko cihema cokomanako; ndipo dziko linawagoniera.

2 Ndipo anatsala mwa ana a Israyeli mapfuko asanu ndi awiri osawagawira colowa cao.

3 Ndipo Yoswa anati kwa ana a Israyeli, Mucedwa mpaka liti kulowa ndi kulandira dziko limene Yehova Mulungu wa makolo anu anakupatsani?

4 Mudzifunire amuna, pfuko liri lonse amuna atatu; kuti ndiwatume, anyamuke, nayendeyende iwo pakati pa dziko, nalilembe monga mwa colowa cao; nabwereoso kwa ine.

5 Ndipo adzaligawa magawo asanu ndi awiri; Yuda adzakhala m'malire ace kumwela, ndi a m'nyumba ya Yosefe adzakhala m'malire mwao kumpoto.

6 Ndipo muzilemba dziko likhale magawo asanu ndi awiri, ndi kubwera nao kuno kwa ine malembo ace; ndipo ndidzakuloterani maere pane pamaso pa Yehova Mulungu wathu.

7 Pakuti Alevi alibe gawo pakati pa inu; pakuti unsembe wa Yehova ndiwo colowa cao. Koma Gadi, ndi Rubeni, ndi pfuko la Manase logawika pakati adalandira colowa cao tsidya lija la Yordano kum'mawa, cimene Mose mtumiki wa Yehova adawapatsa.

8 Ndipo amunawo ananyamuka, namuka; ndipo Yoswa analamulira opita kulemba dzikowo, ndi kuti, Mukani, muyendeyende pakati pa dziko, ndi kulilemba, oimubwerenso kwa ine, ndipo ndidzakuloterani maere pane pamaso pa Yehova pa Silo.

9 Namuka amunawo, napitapita pakati pa dziko, nalilemba m'buku, nayesa midzi yace, magawo asanu, nabwera kwa Yoswa ku cigono ku Silo.

10 Ndipo Yoswa anawalotera maere ku Silo pamaso pa Yehova; ndi apo Yoswa anawagawira ana a Israyeli dziko, monga mwa magawo ao.

Malire a Benjamini

11 Ndipo maere a ana a Benjamini anakwera monga mwa mabanja ao; ndi malire a gawo lao anaturuka pakati pa ana a Yuda ndi ana a Yosefe.

12 Ndipo malire ao a kumpoto anacokera ku Yordano; ndi malire anakwera ku mbali ya Yeriko kumpoto, nakwera pakati pa mapiri kumadzulo; ndi maturukiro ace anali ku cipululu ca Beti-aveni.

13 Ndipo malire anapitirirapo kumka ku Luzi, ku mbali ya Luzi, momwemo ndi Beteli, kumwela; ndi malire anatsikira kumka ku Atarotu-adara, ku phiri lokhala kumwela kwa Betihoroni wa kunsi.

14 Ndipo malire analembedwa nazungulira ku mbali ya kumadzulo kumka kumwela, kucokera ku phiri pokhala patsogolo pa Beti-horoni, kumwela kwace; ndi maturukiro ace anali ku Kiriyatibaala, womwewo ndi Kiriyati-Yearimu, mudzi wa ana a Yuda; ndiyo mbali ya kumadzulo.

15 Ndipo mbali ya kumwela inayambira polekezera Kiriyati-Yearimu; naturuka malire kumka kumadzulo, naturuka kumka ku citsime ca madzi a Nefitoa;

16 natsikira malire kumka polekezera phiri lokhala patsogolo pa cigwa ca mwana wa Hinomu, ndico ca m'cigwa ca Refai kumpoto; natsikira ku cigwa ca Hinomu, ku mbali ya Ayebusi kumwela, natsikira ku Enirogeli;

17 nalembedwa kumka kumpoto, naturuka ku Eni-semesi, naturuka ku Gelilotu, ndiwo pandunji pokwerera pa Adumi; natsikira ku mwala wa Bohani mwana wa Rubeni;

18 napitirira ku mbali ya pandunji pa Araba kumpoto, natsikira kumka ku Araba;

19 napitirira malire kumka ku mbali ya Beti-hogila kumpoto; ndi maturukiro ace a malire anali ku nyondo ya kumpoto ya Nyanja ya Mcere; pa kulekezera kwa kumwela kwa Yordano; ndiwo malire a kumwera.

20 Ndipo malireace mbali ya kum'mawa ndiwo Yordano, ndico colowa ca ana a Benjamini, kunena za malire ace pozungulira pace, monga mwa mabanja ao.

21 Koma midzi ya pfuko la ana a Benjamini monga mwa mabanja ao ndiyo Yeriko, ndi Beti-hogila, ndi Emekikozizi;

22 ndi Beti-araba, ndi Zemaraimu, ndi Beteli;

23 ndi Arimu ndi Para, ndi Ofira;

24 ndi Kefaraamoni, ndi Ofini, ndi Geba; midzi khumi ndi iwiri pamodzi ndi miraga yao;

25 Gibeoni ndi Rama, ndi Beeroti;

26 ndi Mizipe, ndi Kefira, ndi Moza;

27 ndi Rekemu, ndi Iripeeli ndi Tarala;

28 ndi Zela, Elefi, ndi Yebusi, womwewo ndi Yerusalemu, Gibeati ndi Kiriyati; midzi khumi ndi inai pamodzi ndi miraga yace, Ndico colowa ca ana a Benjamini monga mwa mabanja ao.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24