Yoswa 21 BL92

Midzi yokhalamo Alevi

1 Pamenepo akuru a nyumba za atate a Alevi anayandikira kwa Eleazare wansembe, ndi kwa Yoswa mwana wa Nuni, ndi kwa akuru a nyumba za atate a mapfuko a ana a Israyeli;

2 nanena nao ku Silo m'dziko la Kanani, ndi kuti Yehova analamulira mwa dzanja la Mose kuti atipatse midzi yokhalamo ife, ndi mabusa a zoweta zathu.

3 Ndipo ana a Israyeli anapatsa Alevi, kutapa pa colowa cao, monga mwa lamulo la Yehova, midzi iyi ndi mabusa ao.

4 Ndipo maere anaturukira mabanja a Akohati; ndipo molota maere ana a Aroni wansembe, ndiwo Alevi, analandira motapa pa pfuko la Yuda, ndi pa pfuko la Simeoni, ndi pa pfuko la Benjamini, midzi khumi ndi itatu.

5 Ndipo ana otsala a Kohati analandira molota maere motapa pa mabanja a pfuko la Efraimu, ndi pa pfuko La Dani, ndi pa pfuko La Manase logawika pakati, midzi khumi.

6 Ndipo ana a Gerisoni analandira molota maere motapa pa mabanja a pfuko la Isakara, ndi pa pfuko la Aseri, ndi pa pfuko la Nafitali, ndi pa pfuko la Manase logawika pakati m'Basana, midzi khumi ndi itatu.

7 Ana a Merari, monga mwa mabanja ao, analandira motapa pa pfuko la Rubeni, ndi pa pfuko la Gadi, ndi pa pfuko la Zebuloni midzi khumi ndi iwiri.

8 Motero ana a Israyeli anapatsa Alevi midzi iyi ndi mabusa ao, molota maere, monga Yehova adalamulira mwa dzanja la Mose.

9 Ndipo anapatsa motapa pa pfuko la ana a Yuda, ndi pa pfuko la ana a Simeoni, midzi iyi yochulidwa maina ao;

10 kuti ikhale ya ana a Aroni a mabanja a Akohati, a ana a Levi, pakuti maere oyamba adaturukira iwowa.

11 Ndipo anawapatsa mudzi wa Ariba, ndiye atate wa Anoki, womwewo ndi Hebroni, ku mapiri a Yuda, ndi mabusa ace ozungulirapo.

12 Koma minda ya mudzi ndi miraga yace anapatsa Kalebe mwana wa Yefune, ikhale yace.

13 Ndipo kwa ana a Aroni wansembe anapatsa Hebroni ndi mabusa ace, ndiwo mudzi wopulumukirako wakupha mnzace, ndi Libina ndi mabusa ace;

14 ndi Yatiri ndi mabusa ace, ndi Esitimoa ndi mabusa ace;

15 ndi Holoni ndi mabusa ace, ndi Debiri ndi mabusa ace;

16 ndi Aini ndi mabusa ace, ndi Yuta ndi mabusa ace, ndi Betisemesi ndi mabusa ace; midzi isanu ndi inai yotapira mapfuko awiri aja.

17 Ndipo motapira pfuko La Benjamini, Gibeoni ndi mabusa ace, Geba ndi mabusa ace,

18 Anatotu ndi mabusa ace, ndi Alimoni ndi mabusa ace; midzi inai.

19 Miclzi yonse ya ana a Aroni, ansembe, ndiyo khumi ndi itatu, ndi mabusa ao.

20 Ndipo mabanja a ana a Kohati, Aleviwo, otsala a ana a Kohati, analandira midzi ya maere ao motapira pa pfuko la Efraimu.

21 Ndipo anawapatsa Sekemu ndi mabusa ace ku mapiri a Efraimu, ndiwo mudzi wopulumukirako wakupha mnzaceyo, ndi Gezeri ndi mabusa ace;

22 ndi Kibizaimu ndi mabusa ace, Betihoroni ndi mabusa ace; midzi inai.

23 Ndipo motapira m'pfuko La Dani, Eliteke ndi mabusa ace, Gibetoni ndi mabusa ace;

24 Aijaloni ndi mabusa ace, Gati-rimoni ndi mabusa ace; midzi inai.

25 Ndipo motapira pa pfukola Manaselogawika pakati, Taanaki ndi mabusa ace, ndi Gati-rimoni ndi mabusa ace; midzi iwiri.

26 Midzi yonse ya mabanja a ana otsala a Kohati ndiyo khumi ndi mabusa ao.

27 Ndipo anapatsa ana a Gerisoni, a mabanja a Alevi, motapira pa pfuko la Manase logawika pakati, Golani m'Basana ndi mabusa ace, ndiwo mudzi wopulumukirako wakupha mnzaceyo; ndi Beesitera ndi mabusa ace; midzi iwiri.

28 Ndipo motapira pa pfuko la Isakara, Kisioni ndi mabusa ace, Daberati ndi mabusa ace;

29 Yarimutu ndi mabusa ace, Eniganimu ndi mabusa ace; midzi inai.

30 Ndipo motapira pa pfuko La Aseri, Misali ndi mabusa ace, Abidoni ndi mabusa ace;

31 Helikati ndi mabusa ace, ndi Rehobo ndi mabusa ace; midzi inai.

32 Ndipo motapira pa pfuko la Nafitali, Kedesi m'Galileya ndi mabusa ace, ndiwo mudzi wopulumukirako wakupha mnzaceyo, ndi Hamotidori ndi mabusa ace, ndi Karitani ndi mabusa ace, midzi itatu.

33 Midzi yonse ya Agerisoni monga mwa mabanja ao ndiyo midzi khumi ndi itatu ndi mabusa ao.

34 Ndipo anapatsa kwa mabanja a ana a Merari, otsala a Alevi, motapira pa pfuko la Zebuloni, Yokineamu ndi mabusa ace, ndi Karita ndi mabusa ace,

35 Dimna ndi mabusa ace, Nahalala ndi mabusa ace; midzi inai.

36 Ndipo motapira pa pfuko la Rubeni, Bezeri ndi mabusa ace, ndi Yahazi ndi mabusa ace,

37 Kedimotu ndi mabusa ace, ndi Mefati ndi mabusa ace; midzi inai.

38 Ndipo motapira m'pfuko la Gadi, Ramoti m'Gileadi ndi mabusa ace ndiwo mudzi wopulumukirako wakupha mnzaceyo, ndi Mahanaimu ndi mabusa ace;

39 Hesiboni ndi mabusa ace. Yazeri ndi mabusa ace: yonse pamodzi midzi inai.

40 Yonseyi ndiyo midzi ya ana a Merari monga mwa mabanja ao, ndiwo otsala a mabanja a Alevi; ndipo gawo lao ndilo midzi khumi ndi iwiri.

41 Midzi yonse ya Alevi, pakati pa colowa ca ana a Israyeli ndiyo midzi makumi anai kudza isanu ndi itatu, ndi mabusa ao.

42 Midzi iyi yonse inali nao mabusa ao pozungulira pao: inatero midzi iyi yonse.

43 Motero Yehova anawapatsa Israyeli dziko lonse adalumbiralo kuwapatsa makolo ao: ndipo analilandira lao lao, nakhala m'mwemo.

44 Ndipo Yehova anawapatsa mpumulo pozungulira ponse, monga mwa zonse adalumbirira makolo ao; ndipo pamaso pao sipanaima munthu mmodzi wa adani ao onse; Yehova anapereka adani ao onse m'manja mwao.

45 Sikadasowa kanthu konse ka zinthu zokoma zonse Yehova adazinenera nyumba ya Israyeli; zidacitika zonse.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24