1 Pamenepo Yoswa anaitana Arubeni ndi Agadi, ndi pfuko la Manase logawika pakati,
2 nanena nao, Mwasunga inu zonsezo anakulamulirani Mosemtumiki wa Yehova; mwamveranso mau anga m'zonse ndinakulamulirani inu;
3 simunasiya abale anu masiku awa ambiri mpaka lero lino, koma mwasunga cisungire lamulola Yehova Mulungu wanu.
4 Ndipo tsopano Yehova Mulungu wanu wapumitsa abale anu, monga adanena nao; potero bwererani tsopano, mu kani ku mahema anu, ku dziko la colowa canu cimene Mose mtumiki wa Yehova anakuninkhani tsidya lija la Yordano.
5 Koma samalirani bwino kuti mucite cilangizo ndi cilamulo zimene Mose mtumiki wa Yehova anakulamulirani kukonda Yehova Mulungu wanu, ndi kuyenda m'njira zace zonse ndi kusunga malamulo ace, ndi kumuumirira iye, ndi kumtumikira iye ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse.
6 Momwemo Yoswa anawadalitsa, nawauza amuke; ndipo anamuka ku mahema ao.
7 Ndipo gawo limodzi la pfuko la Manase, Mose anawapatsa colowa m'Basana; koma gawo lina Yoswa anawaninkha colowa pakati pa abale ao tsidya lija la Yordano kumadzulo. Ndiponso pamene Yoswa anawauza amuke ku mahema ao, anawadalitsa;
8 nanena nao ndi kuti, Bwererani naco cuma cambiri ku mahema anu, ndi zoweta zambirimbiri, ndi siliva, ndi golidi, ndi mkuwa, ndi citsulo, ndi maraya ambirimbiri; mugawane nao abale anu zofunkha kwa adani anu.
9 Ndipo ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi pfuko la Manase logawika pakati anabwerera, nacoka kwa ana a Israyeli ku Silo, ndiwo wa m'dziko la Kanani kumka ku dziko la Gileadi, ku dziko lao lao, limene anakhala eni ace, monga mwa lamulo la Yehova, mwa dzanja la Mose.
10 Ndipo pamene anafikira mbali ya ku Yordano, ndilo la m'dziko la Kanani, ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi pfuko la Manase logawika pakati anamanga ku Yordano guwa la nsembe, guwa lalikuru maonekedwe ace.
11 Ndipo ana a Israyeli anamva anthu akuti, Taonani ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi pfuko la Manase logawika pakati anamanga guwa la nsembe pandunji pa dziko la Kanani, ku mbali ya ku Yordano, ku mbali ya ana a Israyeli.
12 Pamene ana a Israyeli anamva ici msonkhano wonse wa ana a Israyeli anasonkhana ku Silo, kuti awakwerere kuwathira nkhondo.
13 Ndipo ana a Israyeli anatumiza kwa ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi pfuko la Manase logawika pakati, ku dziko la Gileadi, Pinehasi mwana wa Eleazare wansembe,
14 ndi akalonga khumi naye; nyumba imodzi ya atate kalonga mmodzi, kotero ndi mapfuko onse a Israyeli; yense wa iwowa ndiye mkuru wa nyumba ya atate ao mwa mabanja a Israyeli.
15 M'mene anafika kwa ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi pfuko la Manase logawika pakati, ku dziko la Gileadi, ananena nao ndi kuti,
16 Utero msonkhano wonse wa Yehova, Colakwa ici nciani mwalakwira naco Mulungu wa Israyeli, ndi kumtembenukira Yehova lero line kusamtsatanso, popeza munadzimangira guwa la nsembe kupikisana ndi Yehova lero lino?
17 Kodi mphulupulu ya ku Peori iticepera, imene sitinadziyeretsera mpaka lero lino, ungakhale mliri unadzera msonkhano wa Yehova,
18 kuti mubwerera lero line kusatsata Yehova? ndipo kudzakhala kuti popeza lero mupikisana ndi Yehova, mawa adzakwiyira msonkhano wonse wa Israyeli.
19 Koma mukayesa dziko La colowa canu ncodetsa, olokani kulowa m'dziko lacolowaca Yehova m'mene cihemaca Yehovacikhalamo, nimukhale naco colowa pakati pa ife; koma musapikisana ndi Yehova kapena kupikisana nafe, ndi kudzimangira nokha guwa la nsembe, pamodzi ndi guwa la nsembe la Yehova Mulungu wathu.
20 Kodi Akani mwana wa Zera sanalakwa m'coperekedwaco, ndipo mkwiyo unagwera msonkhano wonse wa Israyeli? osangoonongeka yekha munthuyo mu mphulupulu yace.
21 Pamenepo ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi pfuko la Manase logawika pakati anayankha, nanena ndi akuru a mabanja a Israyeli,
22 Yehova Cauta Mulungu, Yehova Cauta Mulungu, iye adziwa, ndi Israyeli adzadziwa; ngati mopikisana, ngati molakwira Yehova,
23 tadzimangira guwa la nsembe, kubwerera kusamtsata Yehova, musatipulumutsa lero lino; kapena ngati kufukizapo nsembe yopsereza, kapena nsembe yaufa, kapena kuperekapo nsembe zoyamika, acifunse Yehova mwini wace;
24 ndipo ngati ife sitinacita ici cifukwa ca kuopa mlandu, ndi kuti, Masiku akudzawo ana anu akadzanena ndi ana athu, ndi kuti, Muli ciani inu kwa Yehova Mulungu wa Israyeli?
25 pakuti Yehova anaika Yordano ukhale malire pakati pa ife ndi inu, ana a Rubeni, ndi ana a Gadi; mulibe gawo ndi Yehova; motero ana anu adzaleketsa ana athu asaope. Yehova.
26 Cifukwa cace tinati, Tiyeni tikonzeretu zotimangira guwa la nsembe, si kufukizapo nsembe yopsereza ai, kapena nsembe yophera ai;
27 koma lidzakhala mboni pakati pa ife ndi inu; ndi pakati pa mibadwo yathu ya m'tsogolo, kuti tikacita nchito ya Yehova pamaso pace ndi nsembe zathu zopsereza, ndi zophera, ndi zoyamika; kuti ana anu asanene ndi ana athu m'tsogolomo, Mulibe gawo ndi Yehova.
28 Cifukwa cace tinati, Kudzali, akadzatero kwa ife, kapena kwa mibadwo yathu m'tsogolomo, kuti tidzati, Tapenyani, citsanzo ca guwa la nsembe la Yehova, comanga makolo athu, si kufukizapo nsembe yopsereza ai, kapena nsembe yophera ai, koma ndilo mboni pakati pa ife ndi inu.
29 Sikungatheke kuti tipikisane ndi Yehova ndi kubwerera lero kusatsata Yehova, kumanga guwa la nsembe la kufukizapo nsembe yopsereza, la nsembe yaufa, kapena yophera, pamodzi ndi guwa la nsembe la Yehova Mulungu wathu lokhala pakhomo pa cihema cace.
30 Pamene Pinehasi wansembe, ndi akalonga a msonkhano ndi akuru a mabanja a Israyeli okhala naye anamva mau adawanena ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi ana a Manase, anawakomera pamaso pao.
31 Ndipo Pinehasi, mwana wa Eleazare wansembe ananena ndi ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi ana a Manase, Lero lino tidziwa kuti Yehova ali pakati pa ife, pakuti simunalakwira naco Yehova; tsopano mwalanditsa ana a Israyeli m'dzanja la Yehova.
32 Ndipo Pinehasi mwana wa Eleazare wansembe, ndi akalonga anabwerera kucokera kwa ana a Rubeni, ndi kwa ana a Gadi, m'dziko la Gileadi, kudza ku dziko La Kanani kwa ana a Israyeli, nawabwezera mau.
33 Ndipo mauwo anakomera ana a Israyeli pamaso pao; ndi ana a Israyeli analemekeza Mulungu, osanenanso za kuwakwerera ndi kuwathira nkhondo, kuliononga dziko lokhalamo ana a Rubeni ndi ana a Gadi.
34 Ndipo ana a Rubeni ndi: ana a Gadi analicha guwa la nsembelo: Ndilo mboni pakati pa ife kuti Yehova ndiye Mulungu.