Yoswa 9 BL92

1 Yoswa anyengedwa ndi Agibeoni napangana nao. Ndipo kunali, pakumva ici mafumu onse a tsidya ilo la Yordano, kumapiri ndi kucidikha, ndi ku madoko onse a nyanja yaikuru, pandunji pa Lebano: Ahiti ndi Aamori, Akanani, Aperizi, Ahivi, ndi Ayebusi;

2 anasonkhana kuponyana ndi Yoswa ndi Israyeli, ndi mtima umodzi.

3 Koma pamene nzika za Gibeoni zinamva zimene Yoswa adacitira Yeriko ndi Ai,

4 zinacita momcenierera, nizimuka nizioneka ngati mithenga, nizitenga matumba akale pa aburu ao, ndi matumba a vinyo akale ndi ong'ambika ndi omangamanga;

5 ndi nsapato zakale za zigamba pa mapazi ao, nizibvala nsanza; ndi mikate yonse ya kamba wao inali youma ndi yoyanga nkhungu.

6 Ndipo zinamuka kwa Yoswa kumisasa ku Giligala, niziti kwa iye ndi kwa amuna a Israyeli, Tacokera dziko lakutali, cifukwa cace mupangane nafe.

7 Ndipo amuna a Israyeli anati kwa Ahivi, Kapena mulimkukhala pakati pa ife, ndipo tipanganenji ndi inu?

8 Koma anati kwa Yoswa, Ndife akapolo anu. Pamenepo Yoswa anati kwa iwo, Ndinu ayani? ndipo mufuma kuti

9 Ndipo anati kwa iye, Akapolo anu afumira dziko la kutalitali, cifukwa lea dzina la Yehova Mulungu wanu; pakuti tidamva mbiri yace, ndi zonse anacita m'Aigupto,

10 ndi zonse anacitira mafumu awiri a Aamori okhala tsidya lija la Yordano, Sihoni mfumu ya ku Hesiboni, ndi Ogi mfumu ya ku Basana wokhala ku Asitorotu.

11 Ndipo akuru athu ndi nzika zonse za m'dziko mwathu zidanena nafe ndi kuti, Mutenge m'dzanja lanu kamba wa paulendo, kakomane naoni, nimunene nao, Ndife akapolo anu; ndipo tsopano mupangane nafe.

12 Mkate wathu uwu tinadzitengera kamba m'nyumba zathu, ukali wamoto, tsiku loturuka Ife kudza kwanu kuno; koma tsopano, taonani, uli wouma ndi woyaoga nkhungu;

13 ndi matumba a vinyo awa tinawadzaza akali atsopano; ndipo taonani, ang'ambika; ndi malaya athu awa ndi nsapato zathu zatha, cifukwa ca ulendo wocokera kutali ndithu.

14 Pamenepo amunawo analandirako kamba wao, osafunsira pakamwa pa Yehova.

15 Ndipo Yoswa anacitirana nao mtendere, napangana nao, akhale amoyo; ndi akalonga a msonkhano anawalumbirira,

16 Ndipo kunali, atatha kupangana nao masiku atatu, anamva kuti ndiwo anansi ao, ndi kuti kwao ndi pakati pao,

17 Ndipo ana a Israyeli anayenda ulendo, nafika ku midzi yap tsiku lacitatu. Koma midzi yao ndiyo Gibeoni, ndi Cefira, ndi Beerotu ndi KiriyatuYearimu.

18 Ndipo ana a Israyeli sanawakantha, pakuti akalonga a msonkhano adawalumbirira kwa Yehova, Mulungu wa Israyeli. Ndipo msonkhano wonse unadandaula pa akalonga,

19 Koma akalonga onse ananena kwa msonkhano wonse, Tinawalumbirira kwa Yehova Mulungu wa Israyeli, m'mwemo sitikhoza kuwacitira kanthu.

20 Tidzawacitira ici, ndi kuwasunga amoyo; ungatigwere mkwiyo cifukwa ca lumbirolo tidawalumbirira.

21 Ndipo akalonga ananena nao, Akhale ndi moyo; ndipo anasanduka akutema nkhuni, ndi otungira madzi msonkhano wonse; monga akalonga adanena nao.

22 Ndipo Yoswa anawaitana, nanena nao, kuti, Mwatinyenga cifukwa ninji, ndi kuti, Tikhala kutaritari ndi inu, pokhala kwanu kuli pakati pa ife?

23 Ndipo tsopano mukhale otembereredwa, palibe mmodzi wa inu adzamasuka wosakhala kapolo, ndi kutemera nkhuni, ndi kutungira madzi nyumba ya Mulungu wanga.

24 Ndipo anamyankha Yoswa nati, Popeza anatiuzitsa akapolo anu kuti Yehova Mulungu wanu analamulira mtumiki wace Mose kukupatsani dziko lonseli, ndi kupasula nzika zonse za m'dziko pamaso panu; potero tinaopera kwambiri moyo wathu pamaso panu, ndipo tinacita cinthuci.

25 Ndipo tsopano, taonani, tiri m'dzanja lanu; monga muyesa cokoma ndi coyenera kuticitira ife, citani.

26 Pamenepo anawacitira cotero, nawalanditsa m'dzanja la ana a Israyeli, angawaphe.

27 Ndipo tsiku lija Yoswa anawasandutsa akutema nkhuni, ndi otungira madzi msonkhanowo, ndi guwa la nsembe la Yehova, mpaka lero lino, pamalopo akadzasankha.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24