Yoswa 1 BL92

1 NDIPO atafa Mose mtumiki wa Yehova, Yehova anati kwa Yoswa mwana wa Nuni mnyamata wa Mose,

2 Mose mtumiki wanga wafa; tauka tsono, nuoloke Yordano uyu, iwe ndi anthu awa onse, kulowa m'dzikomo ndirikuwapatsa, ndiwo ana a Israyeli.

3 Pali ponse phazi lanu lidzapondapo ndinakupatsani, monga ndinanena ndi Mose.

4 Kuyambira cipululu, ndi Lebano uyu, kufikira mtsinje waukulu mtsinje wa Firate, dziko lonse la Ahiti, ndi kufikira nyanja yaikuru ku malowero a dzuwa, ndiwo malire anu.

5 Palibe munthu adzatha kuima pamaso pako masiku onse a moyo wako; monga ndinakhala ndi Mose momwemo ndidzakhala ndi iwe; sindidzakusowa, sindidzakusiya.

6 Khala wamphamvu, nulimbike mtima, pakuti udzagawira anthu awa dzikoli likhale colowa cao, ndilo limene ndinalumbirira makolo ao kuwapatsa.

7 Komatu khala wamphamvu, nulimbike mtima kwambiri, kuti usamalire kucita monga mwa cilamulo conse anakulamuliraco Mose mtumiki wanga; usacipambukire ku dzanja lamanja kapena kulamanzere, kuti ukacite mwanzeru kuli konse umukako.

8 Buku ili la cilamulo lisacoke pakamwa pako; koma ulingiriremo usana ndi usiku, kuti usamalire kucita monga mwa zonse zolembedwamo; popeza ukatero udzakometsa njira yako, nudzacita mwanzeru.

9 Kodi sindinakulamulira iwe? Khala wamphamvu, nulimbike mtima, usaope, kapena kutenga nkhawa, pakuti Yehova Mulungu wako ali ndi iwe kuli konse umukako.

10 Pamenepo Yoswa analamulira akapitao a anthu, ndi kuti,

11 Pitani pakati pa cigono, nimulamulire anthu, ndi kuti, Mudzikonzeretu kamba, pakuti asanapite masiku atatu mudzaoloka Yordano uyu, kulowa ndi kulandira dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani, likhale lanu lanu.

12 Ndipo Yoswa anati kwa Arubeni, ndi Agadi, ndi pfuko la Manase logawika pakati, ndi kuti,

13 Kumbukilani mau amene Mose mtumiki wa Yehova anakulamulirani inu, kuti, Yehova Mulungu wanu akupatsani mpumulo, nadzakupatsani dziko lino.

14 Akazi anu, ana anu, ndi zoweta zanu zikhale m'dzikoli anakuninkhani Mose, tsidya lino la Yordano; koma inu muoloke okonzeka kunkhondo pamaso pa abale anu, ngwazi zonse, ndi kuwathandiza;

15 mpaka Yehova atapatsa abale anu mpumulo, monga umo anakuninkhirani inu, naonso alandira dzikolo awaninkha Yehova Mulungu wanu; pamenepo mubwerere ku dziko lanu lanu, ndi kukhala nalo, limene Mose mtumiki wa Yehova anakupatsani tsidya lino la Yordano la kum'mawa,

16 Ndipo anamyankha Yoswa, nati, Zonse mwatilamulira tidzacita, ndipo kuli konse mutitumako tidzamuka.

17 Monga momwe tinamvera mau onse a Mose momwemo tidzamvera inu; komatu akhale ndi inu Yehova Mulungu wanu monga anakhala ndi Mose.

18 Ali yense wakupikisana ndi inu, osamvera mau anu muli monse mukamlamulira, aphedwe; komatu khalani wamphamvu, nimulimbike mtima.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24