Yoswa 4 BL92

Aimiritsa miyala 12 ikhale cikumbutso ku Giligala

1 Ndipo kunali, utatha kuoloka Yordano mtundu wonse, Yehova ananena ndi Yoswa, nati,

2 Mudzitengere mwa anthu, amuna khumi ndi awiri, pfuko limodzi mwamuna mmodzi;

3 ndipo muwalamulire iwo ndi kuti, Mudzitengere pano pakati pa Yordano, poimapo mapazi a ansembe, miyala khumi ndi iwiri, ndi kuoloka nayo, ndi kulika m'mogona m'mene mugonamo usiku uno.

4 Pamenepo Yoswa anaitana amuna khumi ndi awiriwo amene anawaikiratu mwa ana a Israyeli, pfuko limodzi mwamuna mmodzi;

5 nanena nao Yoswa, Olokani, kutsogolera likasa la Yehova Mulungu wanu pakati pa Yordano, nimudzisenzere yense mwala paphewa pace, monga mwa kuwerenga kwa mapfuko a ana a Israyeli;

6 kuti ici cikhale cizindikilo pakati pa inu. Akakufunsani ana anu m'tsogolomo, ndi kuti, Miyala iyi nja ciani ndi inu?

7 munene nao, Cifukwa madzi a Yordano anadulidwa patsogolo pa likasa la cipangano ca Yehova; muja lidaoloka Yordano, madzi a Yordano anadulidwa; ndipo miyala iyi idzakhala cikumbutso ca ana a Israyeli cikhalire.

8 Ndipo ana a Israyeli anacita monga Yoswa anawalamulira, nasenza miyala khumi ndi iwiri pakati pa Yordano, monga Yehova adalankhula ndi Yoswa, monga mwa kuwerenga kwa mapfuko a ana a Israyeli; ndipo anaoloka nayo kumka kogona, naiika komweko.

9 Ndipo Yoswa anaimika miyala khumi ndi iwiri pakati pa Yordano, poimapo mapazi a ansembe akusenza likasa la cipangano; ikhala komweko kufikira lero lino.

10 Pakuti ansembe akusenza likasa anaima pakati pa Yordano, mpaka zitatha zonse Yehova adazilamulira Yoswa anene kwa anthu, monga mwa zonse Mose adalamulira Yoswa; ndipo anthu anafulumira kuoloka.

11 Ndipo kunali, atatha kuoloka anthu onse, likasa la Yehova linaoloka, ndi ansembe, pamaso pa anthu.

12 Ndipo ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi gawo lija la pfuko la Manase anaoloka ndi zida zao pamaso pa ana a Israyeli, monga Mose adanena nao;

13 ngati zikwi makumi anai ankhondo okonzeka anaoloka pamaso pa Yehova kuthira nkhondo ku zidikha za Yeriko.

14 Tsiku lomwelo Yehova anakulitsa Yoswa pamaso pa Aisrayeli onse; ndipo anamuopa monga anaopa Mose, masiku onse amoyowace.

15 Ndipo Yehova anati kwa Yoswa,

16 Lamulira ansembe akusenza likasa la umboni, kuti akwere kuturuka m'Yordano.

17 Pamenepo Yoswa analamulira ansembe, ndi kuti, Kwerani kuturuka m'Yordano.

18 Ndipo kunali, atakwera ansembe akusenza likasa la cipangano la Yehova, kuturuka pakati pa Yordano, nakwera pamtunda mapazi a ansembe, madzi a m'Yordano anabwera m'njira mwace, nasefuka m'magombe ace onse monga kale.

19 Ndipo anthu anakwera kuturuka m'Yordano tsiku lakhumi la mwezi woyamba, namanga misasa ku Giligala, mbali ya ku m'mawa kwa Yeriko.

20 Ndipo Yoswa anaimika ku Giligala miyala ija khumi ndi iwiri adaitenga m'Yordano.

21 Ndipo anati kwa ana a Israyeli, Ana anu akadzafunsa atate ao masiku akudza, ndi kuti, Miyala iyi nja ciani?

22 pamenepo muzidziwitsa ana anu, ndi kuti, Israyeli anaoloka Yordano uyu pouma.

23 Pakuti Yehova Mulungu wanu anaphwetsa madzi a Yordano pamaso panu, mpaka mutaoloka; monga Yehova Mulungu wanu anacitira Nyanja Yofiira, imene anaiphwetsa pamaso pathu, mpaka titaoloka;

24 kuti mitundu yonse ya pa dziko lapansi idziwe dzanja la Yehova, kuti ndilo lamphamvu; kuti lope Yehova Mulungu wanu masiku onse.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24