Yoswa 8 BL92

Kupasulidwa kwa Ai

1 Pamenepo Yehova anati kwa Yoswa, Usaope, kapena kutenga nkhawa, tenga anthu onse a nkhondo apite nawe, ndipo tauka, kwera ku Ai; taona, ndapereka m'dzanja lako mfumu ya ku Ai, ndi anthu ace ndi mudzi wace ndi dziko lace;

2 ndipo uzimcitira Ai ndi mfumu yace monga umo unamcitira Yeriko ndi mfumu yace; koma zofunkha zace ndi ng'ombe zace mudzifunkhire nokha; udziikire anthu aja lire kukhonde kwa mudzi.

3 Pamenepo anauka Yoswa, ndi anthu onse a nkhondo, kuti akwere ku Ai; ndipo Yoswa anasankha amuna zikwi makumi atatu, ndiwo ngwazi, nawatumiza apite usiku,

4 nawalamulira ndi kuti, Taonani, muzikhala olalira kukhonde kwa mudzi; musakhalira kutali ndi mudzi, koma mukhale okonzekeratu nonse;

5 ndipo ine, ndi anthu onse ali nane, tidzayandikira mudzi; ndipo kudzali, pamene aturuka kudzakomana nafe, monga poyamba paja, tidzathawa pamaso pao;

6 ndipo adzaturuka kutitsata mpaka tidawakokera asiyane ndi mudzi; pakuti adzanena, Atithawa pamaso pathu monga poyamba pala; nafenso tidzathawa pamaso pao;

7 pamenepo muziuka m'molalira ndi kulowa m'mudzi; pakuti Yehova Mulungu wanu adzaupereka m'manja mwanu.

8 Ndipo kudzali, mutagwira mudzi, muzitentha mudziwo ndi moto; muzicita monga mwa mau a Yehova; taonani, ndakulamulirani.

9 Ndipo Yoswa anawatuma, namuka iwo kulowa m'molalira, nakhala pakati pa Beteli ndi Ai, kumadzulo kwa Ai; koma Yoswa anakhala mwa anthu usiku uja.

10 Ndipo Yoswa analawira mamawa, nayesa anthu, nakwera, iye ndi akuru a Israyeli, pamaso pa anthu a ku Ai.

11 Ndi anthu onse a nkhondo okhala naye anakwera, nayandikira nafika pamaso pa mudzi, namanga misasa kumpoto kwa Ai; koma pakati pa iye ndi Ai panali cigwa.

12 Ndipo anatenga amuna ngati zikwi zisanu, nawaika m'molalira pakati pa Beteli ndi Ai, kumadzulo kwa mudzi.

13 Momwemo anaika anthu, khamu lonse lokhala kumpoto kwa mudzi, ndi olalira ao kumadzulo kwa mudzi, ndipo usiku uja Yoswa analowa pakati pa cigwa,

14 Ndipo kunali, pamene mfumu ya ku Ai anaciona, anafulumira iwo, nalawira mamawa, naturuka amuna a m'mudzi kuthirana ndi Israyeli, iye ndi anthu ace onse, poikidwiratu patsogolo pa cidikha; popeza sanadziwa kuti amlalira kukhonde kwa mudzi.

15 Ndipo Yoswa ndi Aisrayeli onse anaoneka ngati a ku Ai alikuwathyola, nathawira njira ya kucipululu.

16 Pamenepo anthu onse okhala m'mudzi, anaitanidwa awapitikitse, nampitikitsa Yoswa, nakokedwa kusiyana ndi mudzi.

17 Ndipo sanatsala mwamuna mmodzi yense m'Ai kapena m'Beteli osaturukira kwa Israyeli; nasiya mudzi wapululu, napitikitsa Israyeli.

18 Pamenepo Yehova anati kwa Yoswa, Tambasula nthungo iri m'dzanja lako iloze ku Ai, pakuti ndidzaupereka m'dzanja lako. Ndipo Yoswa anatambasula nthungoyo inali m'dzanja lace kuloza mudzi.

19 Nauka msanga olalirawo m'mbuto mwao, nathamanga pamene anatambasula dzanja lace, nalowa m'mudzi, naugwira; nafulumira nayatsa mudziwo.

20 Pamene amuna a ku Ai anaceuka, anapenya, ndipo taonani, utsi wa mudzi unakwera kumwamba; nasowa mphamvu iwo kuthawa cakuno kapena cauko; ndi anthu othawira kucipululu anatembenukira owapitikitsa.

21 Ndipo pakupenya Yoswa ndi Israyeli yense kuti olalirawo adagwira mudzi, ndi kuti utsi wa mudzi unakwera, anabwerera, nawapha amuna a ku Ai.

22 A kumudzinso anawaturukira; potero anakhala pakati pa Israyeli, ena mbali yina, ena mbali yina; ndipo anawakantha, mpaka sanatsala kapena kupulumuka wa iwo ndi mmodzi yense.

23 Koma mfumu ya ku Ai anamgwira wamoyo, nadza naye kwa Yoswa.

24 Ndipo kunali, atatha Israyeli kupha nzika zonse za ku Ai, kuthengo, kucipululu kumene anawapitikitsira, natha onse kugwa ndi lupanga lakuthwa mpaka adathedwa onse, Aisrayeli onse anabwerera ku Ai, naukantha ndi lupanga lakuthwa.

25 Ndipo onse amene adagwa tsiku lija, amuna ndi akazi, ndiwo zikwi khumi ndi ziwiri, anthu onse a ku Ai.

26 Popeza Yoswa sanabweza dzanja lace limene anatambasula nalo nthungo, mpaka ataononga konse nzika zonse za ku Ai.

27 Koma ng'ombe ndi zofunkha za mudzi uwu Israyeli anadzifunkhira monga mwa mau a Yehova amene analamulira Yoswa.

28 Ndipo Yoswa anatentha Ai, nausandutsa muunda ku nthawi yonse, bwinja kufikira lero lino.

29 Ndipo mfumu ya ku Ai, anampacika pamtengo mpaka madzulo; koma polowa dzuwa Yoswa analamulira kuti atsitse mtembo wace pamtengo; ndipo anauponya polowera pa cipata ca mudzi; nauniikako mulu waukuru wamiyala, mpaka lero lino.

Apereka nsembe nawerenga Malamulo a Mose ku Ebala ndi Gerizimu

30 Pomwepo Yoswa anamangira Yehova Mulungu wa Israyeli guwa la nsembe m'phiri la Ebala,

31 monga Mose mtumiki wa Mulungu adalamulira ana a Israyeli, monga mulembedwa m'buku la cilamulo ca Mose, guwa la nsembe la miyala yosasema, yoti palibe munthu anakwezapo citsulo; ndipo anafukizirapo Yehova nsembe zopsereza, naphera nsembe zoyamika.

32 Ndipo analembapo pa miyalayi citsanzo ca cilamulo ca Mose, cimene analembera pamaso pa ana a Israyeli.

33 Ndipo Aisrayeli onse, ndi akuru ao, ndi akapitao ao, ndi oweruza ao anaima cakuno ndi cauko ca likasa, pamaso pa ansembe Alevi, akusenza likasa la cipangano la Yehova, mbadwa ndi alendo omwe; ena a iwo pandunji pa phiri la Gerizimu, ndi ena pandunji pa phiri la Ebala; monga Mose, mtumiki wa Yehova, adalamulira poyamba pala kuti adalitse anthu a Israyeli,

34 Atatero, anawerenga mau onse a cilamulo, dalitso ndi temberero, monga mwa zonse zolembedwa m'buku la cilamulo.

35 Panalibe mau amodzi a zonse adazilamulira Mose osawerenga Yoswa pamaso pa msonkhano wonse wa Israyeli, ndi akazi ndi ang'ono, ndi alendo akuyenda pakati pao.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24