1 Ndipo gawo la pfuko la ana a Yuda monga mwa mabanja ao linafikira malire a Edomu, ku cipululu ca Zini kumwera, ku malekezero a kumwera.
2 Ndi malire ao a kumwera, anayambira ku malekezero a Nyanja ya Mcere, ku nyondo yoloza kumwera;
3 naturuka kumwela kwa cikweza ca Akarabi, napitirira ku Zini, nakwera kumwera kwa Kadesi-Barinea, napitirira ku Hezironi, nakwera ku Adara, nazungulira ku Karika;
4 napitirira ku Azimoni, naturuka ku mtsinje wa Aigupto; ndi malekezero a malirewa anali ku Nyanja Yaikuru; awa ndi malire anu a kumwera.
5 Ndi malire a kum'mawa ndiwo Nyanja ya Mcere, mpaka mathiriro ace a Yordano. Ndi malire a kumpoto anayambira nyondo ya nyanja ku mathiriro a Yordano;
6 nakwera malire kumka ku Beti-hogila, napitirira kumpoto kwa Beti-araba; nakwera malire kumka ku mwala wa Bohani mwana wa Rubeni;
7 nakwera malire kumka ku Dibiri, kucokera ku cigwa ca Akori, ndi kumpoto kupenyera Giligala ndiko kundunji kwa cikweza ca Adumi, ndiko kumwela kwa mtsinje; napitirira malire kumka ku madzi a Enisemesi, ndi maturukiro ace anali ku Eni-rogeli;
8 nakwera malire kumka ku cigwa ca mwana wa Hinomu, kumbali kwa Ayebusi, kumwela, ndiko Yerusalemu; nakwera malire kumka kumwamba kwa phiri lokhala patsogolo pa cigwa ca Hinomu kumadzulo, ndilo ku mathero ace a cigwa ca Refai kumpoto,
9 Ndipo analemba malire kuyambira pamwamba pa phiri mpaka citsime ca madzi ca Nefitoa, naturukira malire ku midzi ya phiri la Efroni; ndipo analemba malire kumka ku Baala, ndiwo Kiriyati-Yearimu.
10 Ndipo malire anazungulira kuyambira ku Baala kumka kumadzulo, ku phiri la Seiri, napitirira kumbali kwa phiri la Yearimu kumpoto, ndilo Kesaloni, natsikira ku Beti-semesi, napitirira ku Timina;
11 naturuka malire kumka ku mbali ya Ekroni kumpoto; ndipo analemba malire kumka ku Sikeroni, napitirira ku phiri la Baala, naturuka ku Yabindi; ndipo maturukiro a malire anali kunyanja.
12 Ndi malire a kumadzulo anali ku Nyanja Yaikuru ndiwo malire ace. Awa ndi malire a ana a Yuda pozungulira monga mwa mabanja ao.
13 Koma Yoswa anampatsa Kalebe mwana wa Yefune gawo mwa ana a Yuda, monga Yehova adamlamulira, ndiwo mudzi wa Ariba, ndiye atate wa Anaki, ndiwo Hebroni.
14 Ndipo Kalebe anaingitsako ana amuna atatu a Anaki, ndiwo Sesai, ndi Ahimani, ndi Talimai, ana a Anaki.
15 Nakwera komweko kumka kwa nzika za Dibiri; koma kale dzina la Dibiri ndilo Kiriyati-Seferi.
16 Ndipo Kalebe anati, iye amene akantha Kiriyati-Seferi, naulanda, yemweyo ndidzampatsa Akisa mwana wanga akhale mkazi wace.
17 Ndipo Otiniyeli mwana wa Kenazi, mbale wace wa Kalebe, anaulanda; ndipo anampatsa Akisa mwana wace akhale mkazi wace.
18 Ndipo kunali, m'mene anamdzera, anamkangamiza mwamuna wace kuti apemphe atate wace ampatse munda; ndipo anatsika pa buru; pamenepo Kalebe ananena naye, Ufunanji?
19 Nati iye, Mundipatse dalitso; popeza mwandipatsa dziko la kumwela, ndipatseninso zitsime za madzi. Pamenepo anampatsa zitsime za kumtunda, ndi zitsime za kunsi.
20 Ici ndi colowa ca pfuko la ana a Yuda monga mwa mabanja ao.
21 Ndipo midzi ya ku malekezero a pfuko la ana a Yuda ku malire a Edomu, kumwela ndiwo, Kabizeeli ndi Ederi, ndi Yaguri;
22 ndi Kina ndi Dimona, ndi Adada;
23 ndi Kedesi, ndi Hazori, ndi ltinani;
24 Zifi ndi Telemu ndi Bealoti;
25 ndi Hazorihadata, ndi Kerioti-hezirondi, ndiwo Hazori;
26 Amamu ndi Sema ndi Moloda;
27 ndi Hazara-gada, ndi Hesimoni, ndi Beti-peleti;
28 ndi Hazara-suala, ndi Beereseba, ndi Bizioti;
29 Baala, ndi lyimu, ndi Ezemu;
30 ndi Elitoladi, ndi Kesili ndi Horima;
31 ndi Zikilaga, ndi Madimana ndi Sanasana;
32 ndi Lebaoti, ndi Siliimu, ndi Aini ndi Rimoni; midzi yonse ndiyo makumi awiri kudza isanu ndi inai; pamodzi ndi miraga yao.
33 Ku cigwa, Esitaoli, ndi Zora ndi Asina;
34 ndi Zoona, ndi Eniganimu, Tapua, ndi Enamu;
35 Yarimutu, ndi Adulamu, Soko, ndi Azeka;
36 ndi Saaraimu, ndi Aditaimu, ndi Gedera, ndi Gederotaimu; midzi khumi ndi inai pamodzi ndi miraga yao.
37 Zenani, ndi Hadasa, ndi Migidala-gadi;
38 ndi Dilani, ndi Mizipe, ndi Yokiteeli;
39 Lakisi ndi Bozikatu ndi Egiloni;
40 ndi Kaboni, ndi Lamasi, ndi, Kitilisi;
41 ndi Gaderotu, Beti-dagoni, ndi Naama, ndi Makeda; midzi khumi ndi isanu ndi umodzi pamodzi ndi miraga yao.
42 Libina ndi Eteri ndi Asana;
43 ndi Ifita ndi Asina ndi Nezibi;
44 ndi Kehila ndi Akisibu, ndi Maresa; midzi isanu ndi inai pamodzi ndi miraga yao.
45 Ekroni pamodzi ndi midzi yace ndi miraga yao;
46 kuyambira ku Ekroni mpaka kunyanja, yonse ya ku mbali ya Asidodo, pamodzi ndi miraga yao.
47 Asidodo, midzi yace ndi miraga yace; Gaza, midzi yace ndi miraga yace; mpaka mtsinje wa Aigupto, ndi nyanja yaikuru ndi malire ace.
48 Ndi kumapiri Samiri, ndi Yatiri, om Soko;
49 ndi Dana, ndi Kiriyatisana, ndiwo Dibiri;
50 ndi Anabi, ndi Esitemo, ndi Animu;
51 ndi Goseni, ndi Holoni, ndi Gilo; midzi khumi ndi umodzi pamodzi ndi miraga yao.
52 Arabu, ndi Duma, ndi Esana;
53 ndi Yanimu, ndi Beti-tapua, ndi Apeka;
54 ndi Humita, ndi Kiriyatiariba, ndiwo Hebroni, ndi Ziori; midzi isanu ndi inai pamodzi ndi miraga yao.
55 Maoni, Karimeli, ndi Zifu, ndi Yuta;
56 ndi Yesireeli, ndi Yokideamu, ndi Zoona;
57 Kaini, Gibea ndi Timina; midzi khumi pamodzi ndi miraga yao.
58 Haluli, Beti-zuru, ndi Gedori,
59 ndi Maaratu, ndi Bete-anotu, ndi Elitekoni; midzi isanu ndi umodzi pamodzi ndi miraga yao.
60 Kiriyata-Baala, ndiwo KiriyatiYearimu ndi Raba; midzi iwiri pamodzi ndi miraga yao.
61 M'cipululu, Beti-araba, Midini, ndi Sekaka;
62 ndi Nibisani, ndi Mudzi wa Mcere, ndi En-gedi; midzi isanu ndi umodzi pamodzi ndi miraga yao.
63 Koma ana a Yuda sanakhoza kuingitsa Ayebusi, nzika za Yerusalemu: m'mwemo Ayebusi anakhala pamodzi ndi ana a Yuda, ku Yerusalemu, mpaka lero lino.