1 Ndipo awa ndi mafumu a dzikolo amene ana a Israyeli anwakantha, nalanda dziko lao tsidya la Yordano kum'mawa, kuyambira cigwa ca Arimoni, mpaka phiri la Herimoni, ndi cidikha conse ca kum'mawa;
2 Sihoni mfumu ya Aaroori wokhala m'Hesiboni, wocita ufumu kuyambira ku Aroeri ndiwo m'mphepete mwa cigwa ca Arinoni, ndi pakati pa cigwa ndi pa Gileadi wogawika pakati, kufikira mtsinje wa Yaboki, ndiwo malire a ana a Amoni;
3 ndi pacidikha mpaka nyanja ya Kineroti kum'mawa, ndi mpaka nyanja ya kucidikha, ndiyo Nyanja ya Mcere kum'mawa, njira ya Beti-Yesimoti; ndi kumwela pansi pa matsikiro a Pisiga.
4 Nalandanso malire a Ogi mfumu ya Basana wotsala wa Arefai, wokhala ku Asitarotu ndi ku Edrei,
5 nacita ufumu m'phiri la Herimoni, ndi m'Saleka, ndi m'Basana lonse, mpaka malire a Agesuri, ndi a Maakati, ndi Gileadi wogawika pakati, malire a Sihoni mfumu ya ku Hesiboni.
6 Mose mtumiki wa Yehova ndi ana a Israyeli anawakantha; ndi Mose mtumiki wa Yehova analipereka kwa Arubeni, ndi Agadi ndi pfuko la Manase logawika pakati, likhale colowacao.
7 Ndipo awa ndi mafumu a dzikolo amene Yoswa ndi ana a Israyeli anawakantha tsidya lija la Yordano kumadzulo, kuyambira Baala-gadi m'cigwa ca Lebano mpaka phiri la Halaki lokwera kumka ku Seiri; ndipo Yoswa analipereka kwa mapfuko a Israyeli, likhale lao lao, monga mwa magawo ao;
8 kumapiri ndi kucigwa, ndi kucidikha, ndi kumatsikiro, ndi kucipululu, ndi kumwela: Ahiti, Aamori, ndi Akanani, Aperizi, Ahivi ndi Ayebusi:
9 mfumu ya ku Yeriko, imodzi; mfumu ya ku Ai, ndiwo m'mbali mwa Beteli, imodzi;
10 mfumu ya ku Yerusalemu, imodzi; mfumu ya ku Hebroni, imodzi; mfumu ya ku Yarimutu, imodzi;
11 mfumu ya ku Lakisi, imodzi;
12 mfumu ya ku Egiloni, imodzi; mfumu ya ku Gezere, imodzi;
13 mfumu ya ku Dibiri, imodzi; mfumu ya ku Gederi, imodzi;
14 mfumu ya ku Horima, imodzi; mfumu ya ku Haradi, imodzi;
15 mfumu ya ku Libina, imodzi; mfumu ya ku Adulamu, imodzi;
16 mfumu ya ku Makeda, imodzi; mfumu ya ku Beteli, imodzi;
17 mfumu ya ku Tapuwa, imodzi; mfumu ya ku Heferi, imodzi;
18 mfumu ya ku Afeki, imodzi; mfumu ya ku Lasaroni, imodzi;
19 mfumu ya ku Madoni, imodzi; mfumu ya ku Hazori, imodzi;
20 mfumu ya ku Simironi-meroni, imodzi; mfumu ya ku Akasafu, imodzi;
21 mfumu ya ku Taanaki, imodzi; mfumu ya ku Megido, imodzi;
22 mfumu ya ku Kadesi, imodzi; mfumu ya ku Yokineamu ku Karimeli, imodzi;
23 mfumuya ku Doro, mpaka ponyamuka pa Doro, imodzi; mfumu ya ku Goimu m'Giligala, imodzi;
24 mfumu ya ku Tiriza, imodzi. Mafumu awa onse ndiwo makumi atatu ndi imodzi.