1 Koma ku Yeriko anatseka pazipata, natsekedwa cifukwa ca ana a Israyeli, panalibe woturuka, panalibenso wolowa.
2 Ndipo Yehova ananena kwa Yoswa, Taona, ndapereka m'dzanja lako Yeriko ndi mfumu yace, ndi ngwazi zace.
3 Ndipo muzizungulira mudzi Inu nonse ankhondo, kuuzungulira mudzi kamodzi. Muzitero masiku asanu ndi limodzi.
4 Ndipo ansembe asanu ndi awiri azinyamula mphalasa zisanu ndi ziwiri zanyanga: za nkhosa zamphongo, natsogolere nazo likasa; koma tsiku lacisanu ndi ciwiri muzizungulira mudziwo kasanu ndi kawirio ndi ansembe aziliza mphalasazo.
5 Ndipo kudzakhala kuti akaliza cilizire ndi nyanga ya nkhosa yamphongo, nimumva kulira kwa mphalasa, anthu onse apfuule mpfuu yaikuru; ndipo linga la mudziwo lidzagwa pomwepo, ndi anthu adzakwera ndi kulowamo yense kumaso kwace.
6 Ndipo Yoswa mwana wa Nuni anaitana ansembe, nanena nao, Senzani likasa la cipangano, ndi ansembe asanu ndi awiri anyamule mphalasa zisanu ndi ziwiri zanyanga za nkhosa zamphongo, kutsogolera nazo likasa la Yehova.
7 Nati kwa anthu, Pitani, muzizungulira mudzi, ndi ankhondo ndi zida zao atsogolere likasa la Yehova.
8 Ndipo atanena kwa anthu Yoswa, ansembe asanu ndi awiri akunyamula mphalasa zisanu ndi ziwiri zanyanga za nkhosa zamphongo pamaso pa Yehova, anapita naliza mphalasazo; ndipo likasa la cipangano ca Yehova linawatsata.
9 Ndipo okonzeka kunkhondo anatsogolera ansembe akuliza mphalasa, koma akudza m'mbuyo anatsata likasa, ansembe ali ciombere poyenda iwo.
10 Ndipo Yoswa analamulira anthu, ndi kuti, Musamapfuula, kapena kumveketsa mau anu, asaturuke konse mau m'kamwa mwanu, mpaka tsiku lakunena nanu ine, Pfuulani; pamenepo muzipfuula.
11 Ndipo anazungulitsa likasa la Yehova mudzi, kuzungulira kamodzi; pamenepo analowa kucigono, nagona m'mwemo.
12 Ndipo Yoswa analawira mamawa, ndi ansembe anasenza likasa la Yehova.
13 Ndipo ansembe asanu ndi awiri, akunyamula mphalasa zisanu ndi ziwiri zanyanga za nkhosa zamphongo ndi kutsogolera nazo likasa la Yehova, anayenda ciyendere naliza mphalasazo; ndi okonzeka kunkhondowo anawatsogolera, ndi akudza m'mbuyo anatsata likasa la Yehova, ansembe ali ciombere poyenda iwo.
14 Ndipo tsiku laciwiri anazungulira mudzi kamodzi, nabwera kucigono; anatero masiku asanu ndi limodzi.
15 Ndipo kunali, tsiku lacisanu ndi ciwiri analawira mamawa, mbandakuca, nazungulira mudzi mommuja kasanu ndi kawiri; koma tsiku lijalo anazungulira mudzi kasanu ndi kawiri.
16 Ndipo kunali, pa nthawi yacisanu ndi ciwiri, pamene ansembe analiza mphalasa, Yoswa anati kwa anthu, Pfuulani; pakuti Yehova wakupatsani mudziwo.
17 Koma mudziwo udzaperekedwa kwa Yehova ndi kuonongeka konse, uwu ndi zonse ziri m'mwemo; Rahabi yekha wadamayo adzakhala ndi moyo, iye ndi onse ali naye m'nyumba, cifukwa anabisa mithenga tinawatumawo.
18 Ndipo inu, musakhudze coperekedwaco, mungadziononge konse, potapa coperekedwaco; ndi kuononga konse cigono ca Israyeli ndi kucisautsa.
19 Koma siliva yense, ndi golidi yense, ndi zotengera za mkuwa ndi citsulo zikhala copatulikira Yehova; zilowe m'mosungira cuma ca Yehova.
20 Ndipo anthu anapfuula, naliza mphalasa ansembe; ndipo kunali, pamene anthu anamva kulira kwa mphalasa, anapfuula anthu ndi mpfuu yaikuru, niligwa linga pomwepo; nakwera anthu kulowa m'mudzi, yense kumaso kwace; nalanda mudziwo.
21 Ndipo anapereka kuziononga ndi lupanga lakuthwa zonse za m'mudzi, amuna ndi akazi omwe, ana ndi nkhalamba zomwe, kudza ng'ombe, ndi nkhosa, ndi aburu, ndi lupanga lakuthwa.
22 Ndipo Yoswa ananena kwa amuna awiri anazonda dzikowo, Lowani m'nyumba ya mkazi wadamayo, ndi kuturutsamo mkaziyo ndi zonse ali nazo, monga munamlumbirira iye.
23 Pamenepo anyamata ozondawo analowa, naturutsa Rahabi, ndi atate wace ndi mai wace ndi abale ace, ndi onse anali nao; anaturutsanso acibale ace onse; nawaika kunja kwa cigono ca Israyeli.
24 Ndipo anatentha mudzi ndi moto, ndi zonse zinali m'mwemo; koma siliva ndi golidi ndi zotengera zamkuwa ndi zacitsulo anaziika m'mosungira cuma ca nyumba ya Yehova.
25 Koma Rahabi, mkazi wadamayo ndi banja la atate wace, ndi onse anali nao, Yoswa anawasunga ndi moyo; ndipo anakhala pakati pa Israyeli mpaka lero tino; cifukwa anabisa mithenga imene Yoswa anaituma kuzonda Yeriko.
26 Ndipo Yoswa anawalumbirira nyengo ija, ndi kuti, Wotembereredwa pamaso pa Yehova munthu amene adzauka ndi kumanga mudzi uwu wa Yeriko; adzamanga kuzika kwace ndi kutayapo mwana wace woyamba, nadzaimika zitseko zace ndi kutayapo mwana wace wotsirizira.
27 Potero Yehova anakhala ndi Yoswa; ndi mbiri yace inabuka m'dziko lonse.