Yoswa 14 BL92

Kalebe alandira Hebroni

1 Ndipo awa ndi maiko ana a Israyeli anawalanda m'dziko la Kanani, amene Eleazare wansembe, ndi Yoswa mwana wa Nuni, ndi akulu a nyumba za atate a mapfuko a ana a Israyeli, anawagawira.

2 Kulandira kwao kunacitika ndi kulota maere, monga Yehova adalamulira mwa dzanja la Mose, kunena za mapfuko asanu ndi anai ndi pfuko logawika pakati.

3 Pakuti Mose adapatsa mapfuko awiri, ndi pfuko logawika pakati, colowa tsidya ito la Yordano; koma sanapatsa Alevi colowa pakati pao,

4 Pakuti ana a Yosefe ndiwo mapfuko awiri, Manase ndi Efraimu; ndipo sanawagawira Alevi kanthu m'dziko, koma midzi yokhalamo ndi dziko lozungulirako likhale la zoweta zao ndi cuma cao.

5 Monga Yehova analamulira Mose, momwemo ana a Israyeli anacita, nagawana dziko.

6 Pamenepo ana a Yuda anadza kwa Yoswa ku Giligala; ndi Kalebe mwana wa Yefune Mkenizi ananena naye, Mudziwa cimene Yehova adanena kwa Mose munthu wa Mulungu za ine ndi za inu m'KadesiBarinea.

7 Ndinali ine wa zaka makumi anai muja Mose mtumiki wa Yehova anandituma kucokera ku Kadesi-Barinea, kukazonda dziko; ndipo ndinambwezera mau, monga momwe anakhala mumtima mwanga.

8 Koma abale anga amene anakwera nane anasungunutsa mitima ya anthu; koma ine ndinamtsata Yehova Mulungu wanga ndi mtima wanga wonse.

9 Ndipo Mose analumbira tsiku lomwelo ndi kuti, Zedi, dzikoli phazi lako lapondapo lidzakhala colowa cako, ndi ca ana ako kosalekeza, cifukwa unatsata Yehova Mulungu wanga ndi mtima wonse.

10 Ndipo tsopano, taonani, Yehova anandisunga ndi moyo, monga ananena, zaka izi mak umi anai ndi zisanu kuyambira nthawi ija Yehova ananena kwa Mose mau awa, poyenda Israyeli m'cipululu; ndipo tsopano taonani, ndine wa zaka makumi asanu ndi atatu, kudza zisanu lero lino.

11 Koma lero lino ndiri wamphamvu monga tsiku lija anandituma Mose; monga mphamvu yanga pamene paja, momwemo mphamvu yanga tsopano, kugwira nkhondo, ndi kuturuka ndi kulowa.

12 Ndipo tsopano, ndipatseni phiri ili limene Yehova ananenera tsiku lija; pakuti udamva tsiku lijalo kuti Aanaki anali komweko, ndi midzi yaikuru ndi yamalinga; kapena Yehova adzakhala ndi ine, kuti ndiwaingitse monga ananena Yehova.

13 Pamenepo Yoswa anamdalitsa, napatsa Kalebe mwana wa Yefune Hebroni likhale colowa cace.

14 Cifukwa cace Hebroni likhala colowa cace ca Kalebe mwana wa Yefune Mkenizi mpaka lero lino; popeza anatsata Yehova Mulungu wa Israyeli ndi mtima wonse.

15 Koma kale dzina la Hebroni linali mudzi wa Ariba, ndiye munthu wamkuru pakati pa Aanaki. Ndipo dziko linapumula nkhondo.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24