1 Ndipo amuna a Efraimu anati kwa iye, Ici waticitira nciani, osatiitana popita iwe kulimbana ndi Amidyani? natsutsana naye kolimba.
2 Koma ananena nao, Ndacitanji tsopano monga inu? Kodi kukunkha mphesa kwa Efraimu sikuposa kuchera mphesa kwa Abiezeri?
3 Mulungu anapereka m'dzanja lanu akalonga a Midyani, Orebi ndi Zeebi, ndipo ndinakhoza kucitanji monga inu? Pamenepo mkwiyo wao unamlezera, atanena mau awa.
4 Ndipo Gideoni anafika ku Yordano, naoloka, iye ndi amuna mazana atatu anali naye, ali otopa koma ali cilondolere.
5 Ndipo ananena kwa amuna a ku Sukoti, Mupatsetu anthu awa akunditsata mitanda yamkate; pakuti atopa, ndipo ndirikulondola Zeba ndi Tsalimuna mafumu a Midyani.
6 Koma akalonga a ku Sukoti anati, Kodi manja a Zeba ndi Tsalimuna ali m'dzanja lako tsopano apa, kuti ife tiwaninkhe ankhondo ako mkate?
7 Ndipo Gideoni anati, Cifukwa cace, Yehova akapereka Zeba ndi Tsalimuna m'dzanja langa, ndidzapuntha nyama yanu ndi minga ya m'cipululu ndi mitungwi.
8 Ndipo anacokapo kukwera ku Penueli, nanena nao momwemo; ndipo amuna a ku Penueli anamyankha monga adamyankha amuna a ku Sukoti.
9 Ndipo ananenanso kwa amuna a ku Penueli ndi kuti, Ndikabwerera ndi mtendere ndidzagumula nsanja iyi.
10 Zeba ndi Tsalimuna ndipo anali m'Karikori, ndi a m'misasa ao pamodzi nao, amuna monga zikwi khumi ndi zisanu; ndiwo otsala onse a khamu lonse la ana a kum'mawa; popeza atagwa amuna zikwi zana limodzi ndi makumi awiri akusolola lupanga.
11 Ndipo Gideoni anakwerera njira ya iwo okhala m'mahema kum'mawa kwa Noba, ndi Yogibea, nakantha khamulo popeza khamulo linakhala lokhazikika mtima.
12 Ndipo Zeba ndi Tsalimuna anathawa; koma anawatsata, nagwira mafumu awiri a Midyani Zeba ndi Tsalimuna, nanjenjemeretsa khamu lonse.
13 Pamenepo Gideoni mwana wa Yoasi anabwerera kunkhondo pokwerera pa Heresi.
14 Ndipo anagwira mnyamata wa anthu a ku Sukoti, nafunsira; ndipo anamsimbira akalonga a ku Sukoti, ndi akulu ace amuna makumi asanu ndi awiri kudza asanu ndi awiri.
15 Ndipo anafika kwa amuna a ku Sukoti, nati, Tapenyani Zeba ndi Tsalimuna amene munanditonza nao ndi kuti, Kodi manja a Zeba ndi Tsalimuna akhala m'dzanja lako, kuti tiwaninkhe mkate amuna ako akulema?
16 Ndipo anagwira akulu, a m'mudzi ndi minga ya kucipululu ndi mitungwi, nawalanga nazo amuna a ku Sukoti.
17 Ndipo anagamula nsanja ya Penueli, napha amuna a kumudzi.
18 Pamenepo anati kwa Zeba ndi Tsalimuna, Amunawo munawapha ku Tabori anali otani? Iwo nayankha, Monga iwe momwemo iwowa; yense wakunga mwana wa mfumu.
19 Ndipo anati, Ndiwo abale anga, ana a mai wanga. Pali Yehova mukadawasunga amoyo, sindikadakuphani.
20 Nati kwa Yeteri mwana wace woyamba, Tauka, nuwaphe. Koma mnyamatayo sanasolola lupanga lace; pakuti anaopa, pokhala anali mnyamata.
21 Pamenepo Zeba ndi Tsalimuna anati, Tauka iwe mwini nutigwere; pakuti monga munthu momwemo mphamvu yace. Ndipo Gideoni anauka nawapha Zeba ndi Tsalimuna, nalanda mphande zinali kukhosi kwa ngamila zao.
22 Pamenepo anthu a Israyeli anati kwa Gideoni, Mutilamulire ndi inu, ndi mwana wanu, ndi mdzukulu wanu, pakuti mwatipulumutsa m'dzanja la Amidyani.
23 Koma Gideoni ananena nao. Sindidzalamulira inu, ngakhale mwana wanga sadzalamulira inu; Yehova adzalamulira inu.
24 Gideoni anatinso kwa iwo, Mundilole ndipemphe kanthu kamodzi kwa inu, mundipatse ali yense mapelele mwa zofunkha zanu; pakuti anali nao mapelele agolidi, pokhala anali Aismayeli.
25 Ndipo anayankha, Kupereka tiwapereka; nayalapo cobvala, naponyamo yense mapelele a mwa zofunkha zao.
26 Ndipo kulemera kwace kwa mapelele agolidi adawapempha ndiko masekeli cikwi cimodzi ndi mazana asanu ndi awiri; osawerenga mphande, ndi zitunga ndi zobvala zacibakuwa za pa mafumu a ku Midyani, osawerenganso maunyolo okhala pa makosi a ngamila zao.
27 Ndipo Gideoni anawapanga fano, naliika m'mudzi mwace, ndiwo Ofira; ndi Israyeli yense analitsata kuligwadira pomwepo; ndipo linakhala kwa Gideoni ndi nyumba yace ngati msampha.
28 Motero anagonjetsa Amidyani pamaso pa ana a Israyeli, osaweramutsanso mitu yao iwowa. Ndipo dziko lidapumula zaka makumi anai m'masiku a Gideoni.
29 Ndipo Yerubaala, mwana wa Yoasi anamuka, nakhala, m'nyumba ya iye yekha.
30 Nakhala nao ana amuna makumi asanu ndi awiri Gideoni, anawabala ndi iye; popeza anali nao akazi ambiri.
31 Ndipo mkazi wace wamng'ono wokhala m'Sekemu, iyenso anambalira mwana wamwamuna; namucha dzina lace Abimeleki.
32 Ndipo Gideoni mwana wa Yoasi anafa atakalamba bwino, naikidwa m'manda a Yoasi atate wace, m'Ofira wa Aabiezeri.
33 Ndipo kunali, atafa Gideoni, ana a Israyeli anabwereranso nagwadira Abaala, nayesa Baala-beriti mulungu wao.
34 Ndi ana a Israyeli sanakumbukila Yehova Mulungu wao, amene anawapulumutsa m'dzanja la adani ao onse pozungulira ponse;
35 osacitira cifundo nyumba ya Yerubaala, ndiye Gideoni, monga mwa zokoma zonse iye anacitira Israyeli.