Oweruza 18 BL92

Ana a Dani alanda mafano a Mika

1 Masiku ajawo panalibe mfumu m'Israyeli; masiku ajanso pfuko la Adani anadzifunira colowa cakukhalako; pakuti kufikira tsiku lija sicinawagwera colowa cao pakati pa mapfuko a Israyeli.

2 Ndipo ana a Dani anatuma a banja lao amuna asanu a mwa iwo onse, anthu olimba mtima, a ku Zora, ndi a ku Esitaoli, a kuzonda dziko ndi kufunafunamo; nanena nao, Mukani, mufunefune m'dziko. Nafika iwo ku mapiri a Efraimu ku nyumba ya Mika, nagona komweko,

3 Pokhala iwo m'nyumba ya Mika, anazindikira mau a mnyamata Mleviyo, napambukirako, nanena naye, Anadza nawe kuno ndani? ucitanji muno? ukhala naco ciani kuno?

4 Ndipo ananena nao, Mika anandicitira cakuti cakuti, napangana nane za nchito, ndipo ndikhala wansembe wace.

5 Pamenepo ananena naye, Utifunsire kwa Mulungu, kuti tidziwe ngati ulendo wathu timukawo udzakoma.

6 Nanena nao wansembeyo, Mukani mumtendere, ulendo wanu muyendawo uli pamaso pa Yehova.

7 Pamenepo amuna asanuwa anacoka, nafika ku Laisi; naona anthu anali m'mwemo, kuti anakhalaokhazikika mtima, monga anakhala Asidoni, odekha ndi osatekeseka; popeza m'dzikomo munalibe mwini bwalo wakudtitsa manyazi m'cinthu ciri conse; nasiyana kutali ndi Asidoni, ndipo analibe kanthu ndi munthu ali yense.

8 Ndipo asanuwo anafikanso kwa abale ao ku Zora ndi Esitaoli; ndi abale ao ananena nao, Mutani inu?

9 Nati iwo, Taukani, tiwakwerere; pakuti tapenya dziko, ndipo taonani, ndilo lokoma ndithu; ndi inu muli cete kodi? musamacita ulesi kumuka ndi kulowa kulandira dzikolo,

10 Pomuka inu mudzafikira anthu okhazikika mtima ndi dziko ladtando; pakuti Mulungu walipereka m'dzanja lanu; pamenepo mposasowa kanthu kali konse kali pa dziko lapansi.

11 Pamenepo amuna mazana asanu ndi limodzi, omangira zida za nkhondo m'cuuno, anaphumulako a banja la a Dani, anacokera ku Zora, ndi ku Esitaoli.

12 Nakwera namanga misasa m'Kiriyati-yearimu, m'Yuda; cifukwa cace anacha dzina lace la malowo cigono ca Dani, mpaka lero; taona, ali m'tseri mwa Kiriyatiyearimu.

13 Ndipo anapiririra komweko kumka ku mapiri a Efraimu, nadza ku nyumba ya Mika.

14 Pamenepo anayankha amuna asanu anamukawo kukazonda dziko la Laisi, nanena ndi abale ao, Kodi mudziwa kuti m'nyumba izi muli cobvala ca wansembe, ndi timafano ndi fano losema, ndi fano loyenga? Ndipo tsopano dziwani coyenera inu kucita.

15 Napambuka iwo kumkako, nafika ku nyumba ya mnyamata Mleviyo, ndiyo nyumba ya Mika, namfunsa ngati ali bwanji.

16 Ndipo amuna mazana asanu ndi limodzi omangira zida zao za nkhondo m'cuuno, ndiwo a ana a-Dani, analikuima polowera pa cipata;

17 koma amuna asanu omukawo kukazonda dziko anakwera nalowako, natenga fano losema, ndi cobvala ca wansembe ndi timafano, ndi fano loyenga; ndi wansembe anaima polowera pa cipata pamodzi ndi amuna mazana asanu ndi limodzi omangira zida za nkhondo m'cuuno.

18 Atalowa iwo m'nyumba ya Mika, natengako fane losema, cobvala ca wansembe, ndi timafano, ndi fano loyenga, wansembeyo ananena nao, Mucitanji?

19 Ndipo ananena naye, Khala cete, tseka pakamwa pako, numuke nafe, nutikhalire atate ndi wansembe wathu; cikukomera nciti, kukhala wansembe wa nyumba ya munthu mmodzi, kapena kukhala wansembe wa pfuko ndi banja m'Israyeli?

20 Nukondwera mtima wa wansembeyo, natenga iye cobvala ca wansembe, ndi timafano ndi fano losema, nalowa pakati pa anthu.

21 Atatero anabwerera, nacoka, natsogoza ana ang'ono ndi zoweta ndi akatundu.

22 Atafika kutari ndi nyumba ya Mika, Mikayo anawamemeza amuna a m'nyumba zoyandikizana ndi yace, natsata ndi kuwapeza ana a Dani.

23 Ndipo anapfuula kwa ana a Dani. Naceuka iwo nati kwa Mika, Cakusowa ciani, kuti wamemeza anthu ako?

24 Nati iye, Mwanditengera milungu yanga ndinaipanga, ndi wansembe, ndi kucoka; cinditsaliranso ciani? ndipo muneneranji kwa ine, Cakusowa nciani?

25 Koma ana a Dani anati kwa iye, Mau ako asamveke ndi ife, angakugwere anthu owawa mtima, nukataya moyo wako ndi wa iwo a m'nyumba mwako.

26 Nayenda ulendo wao ana a Dani; ndipo Mika pakuona kuti anamposa mphamvu, anatembenuka nabwerera kunyumba kwace.

27 M'mwemo anatenga zimene Mika adacipanga, ndi wansembe anali naye, nafika ku Laisi, kwa anthu odekha ndi okhazikika mtima, nawakantha ndi lupanga lakuthwa, natentha mudzi wao ndi moto.

28 Ndipo panalibe wolanditsa, popeza ku Sidoni nkutali, ndipo analibe kuyenderana ndi anthu ena; ndiko ku cigwa cokhala ku Betirehobo. Pamenepo anamanganso mudziwo, nakhala m'mwemo.

29 Ndipo analicha dzina la mudziwo Dani, kutsata dzina la atate wao Dani wombala Israyeli; koma poyambapo dzina la mudzi linali Laisi.

30 Ndipo ana a Dani anadziimitsira fane losemalo; ndi Yonatani mwana wa Gerisomu mwana wa Manase, iye ndi ana ace amuna anali ansembe a pfuko la Adani mpaka tsiku lija anatenga ndende anthu a m'dziko.

31 Motero anadziikira fane losema la Mika, limene adalipanga, masiku onse okhala nyumba ya Mulungu ku Silo.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21