1 Koma Abimeleki mwana wa Yerubaala anamuka ku Sekemu kwa abale a amai wace, nanena nao, ndi kwa banja lonse la nyumba ya atate wa amai wace, ndi kuti,
2 Nenanitu m'makutu mwa eni ace onse a ku Sekemu, Cokomera inu nciti, akulamulireni ana amuna onse a Yerubaala ndiwo amuna makumi asanu ndi awiri, kapena akulamulireni mwamuna mmodzi? mukumbukilenso kuti ine ndine wa pfuko lanu ndi nyama yanu.
3 Pamenepo abale a amace anamnenera mau awa onse m'makutu a eni ace onse a Sekemu; ndi mitima yao inalunjika kutsata Abimeleki; pakuti anati, Ndiye mbale wathu.
4 Ndipo anampatsa ndalama makumi asanu ndi awiri za m'nyumba ya Baala-beriti; ndipo Abimeleki analembera nazo anthu opanda pace ndi opepuka amene anamtsata.
5 Ndipo anamuka ku nyumba ya atate wace ku Ofira, nawapha abale ace ana a Yerubaala, ndiwo amuna makumi asanu ndi awiri, pa thanthwe limodzi; koma Yotamu mwana wamng'ono wa Yerubaala anatsalako; pakuti anabisala.
6 Pamenepo anasonkhana eni ace onse a ku Sekemu, ndi nyumba yonse ya Milo, namuka namlonga Abimeleki ufumu pa thundu wa coimiritsa ciri m'Sekemu.
7 Ndipo atamuuza Yotamu, anamuka iye naimirira pamutu pa phiri la Gerizimu, nakweza mau ace, napfuula, nanena nao, Mundimvere ine, eni ace a ku Sekemu inu, kuti Mulungu amvere inu.
8 Kumuka inamuka mitengo kudzidzozera mfumu; niti kwa mtengo waazitona, Ukhale iwe mfumu yathu.
9 Koma mtengo waazitona unati kwa iwo, Ngati ndidzasiya kunona kwanga kumene alemekeza nako Mulungu ndi anthu kukalenga pa mitengo?
10 Pamenepo mitengo inati kwa mkuyu. Tiye iwe, ukhale mfumu yathu.
11 Koma mkuyu unanena nao, Ngati ndidzasiya kuzuna kwanga, ndi zipatso zanga zokoma kukalenga pa mitengo?
12 Pamenepo mitengo inati kwa mpesa, Tiye iwe, ukhale mfumu yathu.
13 Koma mpesa unanena nao, Ngati ndidzasiya vinyo wanga wakusekeretsa Mulungu ndi anthu, kukalenga pa mitengo?
14 Pamenepo mitengo yonse inati kwa nkandankhuku, Tiye iwe, ukhale mfumu yathu.
15 Ndipo nkandankhuku unati kwa mitengo, Mukandidzoza mfumu yanu moonadi, tiyeni, thawirani ku mthunzi wanga; mukapanda kutero uturuke mota m'nkandankhuku ndi kunyeketsa mikungudza ya Lebano.
16 Ndipo tsopano, ngati mwacita moona ndi mwangwiro pakulonga Abimeleki ufumu, ngatinso mwamcitira cokoma Yerubaala ndi nyumba yace, ndi kumcitira monga anayenera manja ace;
17 pakuti atate wanga anakugwirirani nkhondo, nataya moyo wace, nakupulumutsani m'dzanja la Amidyani;
18 koma mwaukira nyumba ya atate wanga lero lino, ndi kuwapha ana ace, ndiwo amuna makumi asanu ndi awiri, pa thanthwe limodzi; ndipo mwalonga Abimeleki mwana wa mdzakazi wace, akhale mfumu ya pa eni ace a ku Sekemu, cifukwa ali mbale wanu;
19 ngati tsono mwacitira Yerubaala ndi nyumba yace zoona ndi zangwiro lero lino, kondwerani naye Abimeleki, nayenso akondwere nanu;
20 koma ngati simunatero, uturuke moto kwa Abimeleki, nunyeketse eni ace a ku Sekemu ndi nyumba ya Milo; nuturuke mota kwa eni ace a ku Sekemu, ndi ku nyumba yace ya Milo, nunyeketse Abimeleki.
21 Pamenepo Yotamu anafulumira, nathawa, namuka ku Beeri, nakhala komweko, cifukwa ca Abimeleki mbale wace.
22 Abimeleki atakhala kalonga wa Israyeli zaka zitatu,
23 Mulungu anatumiza mzimu woipa pakati pa Abimeleki ndi eni ace a ku Sekemu; ndi eni ace a ku Sekemu anamcitira Abimeleki mosakhulupirika;
24 kuti ciwawa adacitira ana amuna makumi asanu ndi awiria Yerubaala cimdzere, ndi kuti mwazi wao uikidwe pa mbale wao Abimeleki anawaphayo, ndi pa eni ace a ku Sekemu, amene analimbikitsa manja ace, awaphe abale ace.
25 Ndipo eni ace a ku Sekemu anaika omlalira pamwamba pa mapiri; amene anawawanya onse akudzera njirayi; ndipo anamuuza Abimeleki.
26 Ndipo Gaala, mwana wa Ebedi anadza ndi abale ace, napita ku Sekemu; ndi eni ace a ku Sekemu anamkhulupirira.
27 Ndipo anaturuka kumka kuminda, nachera mphesa m'mindamo, naponda mphesa, napereka nsembe yolemekeza, nalowa m'nyumba ya mulungu wao, nadya, namwa, natemberera Abimeleki.
28 Pamenepo Gaala, mwana wa Ebedi anati, Abimeleki ndani, ndi Sekemu ndani, kuti timtumikire? sindiye mwana wa Yerubaala kodi? ndi Zebuli kazembe wace? Mutumikire amuna a Hamori atate wa Sekemu; koma ameneyo timtumikire cifukwa ninji?
29 Mwenzi anthu awa akadakhala m'dzanja langa; ndikadamcotsadi Abimeleki. Ndipo anati kwa Abimeleki, Curukitsa khamu lako, nuturuke.
30 Pamene Zebuli woyang'anira mudzi anamva mau a Gaala mwana wa Ebedi, anapsa mtima.
31 Natuma mithenga kwa Abimeleki monyenga nati, Taonani Gaala ndi abale ace afika ku Sekemu; ndipo taonani, akupandukitsirani mudzi.
32 Ndipo tsopano, taukani usiku, inu ndi anthu okhala nanu ndi kulalira kuthengo;
33 ndipo kukhale kuti m'mawa, pakuturuka dzuwa, muuke mamawa mugwere mudziwo; ndipo taonani, akakuturukirani iye ndi anthu ali naye, uzimcitira monga lidziwa dzanja lako.
34 Pamenepo Abimeleki anauka ndi anthu onse anali naye, usiku; nalalira a ku Sekemu, magulu anai.
35 Ndipo Gaala mwana wa Ebedi anaturuka, naima polowera pa cipata ca mudzi; nauka Abimeleki ndi anthu anali naye m'molalira.
36 Ndipo pamene Gaala anapenya anthuwo anati kwa Zebuli, Taona, alikutsika anthu kucokera pamwamba pa mapiri, Koma Zebuli ananena naye, Uona mthunzi wa mapiri ndi kuyesa anthu.
37 Koma Gaala ananenanso, nati, Tapenya alikutsika anthu pakati pa dziko, ndi gulu limodzi lidzera olira ya ku thundu wa alauli.
38 Pamenepo Zebuli anati kwa iye, Pakamwa pako mpoti tsopano, muja udanena, Ndani Abimeleki kud timtumikire? awa si anthuwo unawapeputsa? uturuke tsopano, nulimbane nao.
39 Ndipo Gaala anaturuka pamaso pao pa eni ace a ku Sekemu, nalimbana ndi Abimeleki.
40 Koma Abimeleki anampitikitsa, nathawa iye pamaso pace; nagwa olasidwa ambiri mpaka polowera pa cipata.
41 Ndipo Abimeleki anakhala ku Aruma; ndi Zebuli anafngitsa Gaala ndi abale ace kuti asakhale m'Sekemu.
42 Ndipo kunali m'mawa mwace, kuti anthu anaturuka kumka kuminda; ndipo anauza Abimeleki.
43 Pamenepo anatenga anthu, nawagawa magulu atatu, nalalira m'minda; napenya, ndipo taonani, anthu alimkuturuka m'mudzi; nawaukira iye nawakantha.
44 Ndi Abimeleki ndi magulu okhala naye anathamanga naima polowera pa cipata ca mudzi; ndi magulu awiriwo anagwera onse okhala m'munda, nawakantha.
45 Ndipo Abimeleki analimbana ndi mudzi tsiku lija lonse; nalanda mudzi nawapha anthu anali m'mwemo; napasula mudzi; nawazapo mcere.
46 Ndipo pamene eni ace onse a nsanja ya ku Sekemu anacimva, analowa m'ngaka ya nyumba ya Eliberiti.
47 Ndipo anauza Abimeleki kuti amuna onse a nsanja ya ku Sekemu asonkhane.
48 Pamenepo Abimeleki anakwera kumka ku phiri la Zalimoni, iye ndi anthu onse anali naye; natenga nkhwangwa m'dzanja lace Abimeleki, nadula nthambi kumitengo, nainyamula ndi kulika paphewa pace, nati kwa anthu okhala naye, Ici munaciona ndacita, fulumirani, mucite momwemo.
49 Ndi anthu onse anadulanso yense nthambi yace, natsata Abimeleki, naziika pangaka, natentha nazo ngakayo ndi moto; motero anthu onse a nsanja ya ku Sekemu anafanso, amuna ndi akazi ngati cikwi cimodzi.
50 Pamenepo Abimeleki anamuka ku Tebetsi, naumangira Tebetsi misasa, naulanda.
51 Koma m'mudzimo munali nsanja yolimba nathawira kumeneko amuna ndi akazi onse, ndi eni ace onse a mudziwo, nadzitsekereza m'mwemo, nakwera patsindwi pa nsanja.
52 Ndipo Abimeleki anafika kunsania, nalimbana nayo nkhondo, nayandikira kukhomo kwa nsanja, aitenthe ndi moto.
53 Ndipo mkazi wina anaponya mwana wa mphero pamutu pa Abimeleki, naphwanya bade lace.
54 Pamenepo anaitana msanga mnyamata wace wosenza zida zace, nanena naye, Solola lupanga lako nundiphe, angamanenere anthu, ndi kuti, Anamupha ndi mkazi. Nampyoza mnyamata wace, nafa iye.
55 Pamene amuna a Israyeli anaona kuti adafa Abimeleki anamuka yense kumalo kwace.
56 Momwemo Mulungu anambwezera Abimeleki coipaco anacitira atate wace ndi kuwapha abale ace makumi asanu ndi awiri.
57 Ndipo Mulungu anawabwezera coipa conse ca amuna a ku Sekemu pamitu pao, ndipo linawagwera temberero la Yotamu mwana wa Yerubaala.