1 Ndipo kunali, masiku aja, pamene panalibe mfumu m'Israyeli, panali munthu Mlevi wogonera kutseri kwa mapiri a Efraimu amene anadzitengera mkazi wamng'ono wa ku Betelehemu-Yuda.
2 Koma mkazi wace wamng'ono anacita cigololo akali naye, namcokera kumka ku nyumba ya atate wace ku Betelehemu-Yuda, nakhalako nthawi ya miyezi inai.
3 Koma anauka mwamuna wace namtsata kukamba naye zamtima, kumbwezanso; napita ndi mnyamata wace, ndi aburu awiri. Ndipo mkaziyo anadza naye ku nyumba ya atate wace. Ndipo pakumuona atate wa mkaziyo, anakondwera kukomana naye.
4 Ndipo mpongozi wace, ndiye atate wa mkaziyo, anamuimika kuti akhale naye masiku atatu; nadya namwa nagona komweko.
5 Ndipo kunali, tsiku lacinai, analawirira mamawa, nanyamuka iye kucoka; koma atate wa mkaziyo anati kwa mkamwini wace, Limbitsa mtima wako ndi mkate pang'ono, ndipo utatero upite.
6 Nakhala pansi nadya namwa onse awiri pamodzi; nati kwa munthuyo atate wa mkaziyo, Ubvomere, ugone kuno usiku, nusekerere mtima wako.
7 Ndipo munthuyo ananyamuka kuti amuke; koma mpongozi waceyo anamkakamiza, nagonanso komweko.
8 Nalawirira mamawa tsiku lacisanu kuti amuke, koma atate wa mkaziyo anati, Ulimbitse mtima wako, nulindire lipendeke dzuwa; nadya iwo onse awiri.
9 Pamenepo munthuyo ananyamuka kucoka, iye ndi mkazi wace wamng'ono ndi mnyamata wace; koma mpongozi wace, atate wa mkaziyo, ananena naye, Tapenya, lapendeka dzuwa, ugone kuno usiku; tapenya lapendekatu dzuwa, ugone kuno, nusekerere mtima wako; nimulawire mamawa kumka ulendo wanu kwanu.
10 Koma munthuyo anakana kugonako usiku, nanyamuka, nacoka, nadza pandunji pa Yebusi (ndiwo Yerusalemu); ndi pamodzi naye panali aburu awiri omangirira mbereko; anali nayenso mkazi wace wamng'ono.
11 Pofika iwo pa Yebusi linalimkulowa dzuwa, ndi mnyamata anati kwa mbuye wace, Tiyeni, tipambukire mudzi uwu wa Ayebusi ndi kugona pomwepa.
12 Koma mbuye wace ananena naye, Tisapambukire mudzi wacilendo, wosati wa ana a lsrayeli, koma tipitirire kumka ku Gibeya,
13 Nati kwa mnyamata wace, Tiyeni, tiyandikire kwinako: tigone m'Gibeya, kapena m'Rama.
14 Napitiriraiwo, nayenda, ndi dzuwa linawalowera pafupi pa Gibeya, ndiwo wa Benjamini.
15 Napambukirako, kuti alowe nagone ku Gibeya; nalowa iye, nakhala pansi m'khwalala la mudziwo, pakuti panalibe wina wowalandira m'nyumba agonemo, wakuwapatsa pogona.
16 Ndipo taonani, munthu nkhalamba anacokera ku nchito yace kumunda madzulo; munthuyu ndiye wa ku mapiri a Efraimu, nagonera ku Gibeya; kuma anthu pamenepo ndiwo Abenjamini.
17 Pamene anakweza maso ace anaona munthu wa pa ulendoyo m'khwalala la mudzi; ndi nkhalambayo inati, Umuka kuti? ufumira kuti?
18 Ndipo ananena nayo, Tirikucokera ku BetelehemuYuda, kumka ku mbali za mapiri a Efraimu, ndiko ndifumira ine; koma ndidamuka ku Betelehemu-Yuda; ndipo tsopano ndiri kumuka ku nyumba ya Yehova; koma palibe munthu wondipatsa nyumba.
19 Ngakhale maudzu ndi cakudya ca aburu athu ziriko; ndi mkate ndi vinyo zirikonso kwa ine ndi kwa mdzakazi wako ndi kwa mnyamata wokhala ndi aka polo ako; kosasowa kanthu.
20 Ndipo nkhalambayo inati, Mtendere ukhale ndi iwe, komatu, zosowa zako zonse ndidzakuparsa ndi ine; pokhapo usa gone m'khwalala.
21 Pamenepo anamlonga m'nyumba yace, napatsa aburu cakudya; ndipo iwo anasamba mapazi ao, nadya, namwa.
22 Pokondweretsa iwo mitima yao, taonani amuna a m'mudziwo, ndiwo anthu otama zopanda pace, anazinga nyumba, nagogodagogoda pacitseko; nati kwa mwini nyumba nkhalambayo ndi kuti, Turutsa mwamunayo adalowa m'nyumba mwako kuti timdziwe.
23 Ndipo munthu mwini nyumba anawaturukira nanena nao, lai, abale anga, musacite coipa cotere; popeza mwamuna uyu walowa m'nyumba mwanga, musacite copusa ici.
24 Taonani, mwana wanga wamkazi ndiye namwali, ndi mkazi wace wamng'onoyo siwa; ndiwaturutse iwo, muwacepetse iwo, ndi kuwacitira monga muyesa cokoma; koma mwamuna uyu musamcitire copusa ici.
25 Koma amunawo sanafuna kumvera; motero munthuyu anagwira mkazi wace wamng'ono, naturuka naye kwa iwo kunja; namdziwa iwo, nacita naye zoipa usiku wonse mpaka m'mawa; namlola acoke mbandakuca.
26 Nadza mkaziyo kutaca, nagwa pakhomo pa nyumba ya munthu padali mbuye wace, kufikira kutayera.
27 Pamene mbuye wace anauka mamawa, natsegula pakhomo pa nyumba, naturuka kumka ulendo wace, taona, mkazi wace wamng'onoyo, atagwa pakhomo pa nyumba ndi manja ace paciundo.
28 Ndipo ananena naye, Tauka, timuke; koma panalibe womyankha. Pamenepo anamuika pa buru; nanyamuka mwamunayo, namka kwao.
29 Ndipo pofika iye kunyumba kwace, anatenga mpeni, nagwira mkazi wace wamng'onoyo namgawa ciwalo ciwalo magawo khumi ndi awiri, namtumiza ku mame onse a Israyeli.
30 Ndipo kunali kuti onse amene anaciona anati, Sicinacitika, inde sicinaoneka cotere ciyambire tsiku lokwera ana a Israyeli kuturuka m'dziko la Aigupto mpaka lero lino; lingiriranipo, mupangane nzeru, nimunene.