Oweruza 21 BL92

Pfuko la Benjamini limangidwanso

1 Koma amuna a Israyeli adalumbira ku Mizipa, ndi kuti, Palibe mmodzi wa ife adzapereka mwana wace wamkazi kwa Mbenjamini akhale mkazi wace.

2 Ndipo anthu anadza ku Beteli, nakhala pansi pomwepo pamaso pa Mulungu mpaka madzulo; nakweza mau ao ndi kulira misozi yambiri.

3 Nati iwo, Yehova Mulungu wa Israyeli, cacitika ici cifukwa ninji m'Israyeli kuti lasowa lero pfuko limodzi m'Israyeli?

4 Ndipo kunali m'mawa mwace, anthu analawirira mamawa namangako guwa la nsembe, napereka nsembe zopsereza ndi nsembe zoyamika.

5 Nati ana a Israyeli, Ndani iye mwa mapfuko onse a Israyeli amene sanakwera kudza kumsonkhano kwa Yehova? pakuti panali lumbiro lalikuru pa iye wosakwera kudza kwa Yehova ku Mizipa, ndi kuti, Aphedwe ndithu.

6 Ndipo ana a Israyeli anamva cifundo cifukwa ca Benjamini mbale wao, nati, Pfuko limodzi lalikhidwa pa Israyeli leroli.

7 Tidzatani kuwafunira otsalawo akazi, popeza tinalumbira ife pa Yehova kuti sitidzawapatsa ana athu akazi akhale akazi ao?

8 Nati iwo, Kodi pali lina la mapfuko a Israyeli losakwera kudza kwa Yehova ku Mizipa? Ndipo taonani, kucokera ku Yabesi-gileadi sanadza mmodzi kumisasa, kumsonkhano.

9 Pakuti pamene anawerenga anthu, taonani, panalibe mmodzi komweko wa okhala m'Yabesi-gileadi,

10 Ndipo msonkhano unatumizako amuna zikwi khumi ndi ziwiri, ndiwo ngwazi, nawalamulira ndi kuti, Mukani, nimuwakanthe okhala m'Yabesi-gileadi ndi lupanga lakuthwa, ndi akazi ndi ana ang'ono.

11 Ndipo cimene mukacite ndi ici: mukaononge konse mwamuna ali yense, ndi mkazi ali yense wodziwa mwamuna mogona naye.

12 Ndipo anapeza mwa anthu a Yabesi-gileadi anamwali mazana anai osadziwa mwamuna mogona naye; nabwera nao kumisasa ku Silo, ndiwo a m'dziko la Kanani.

13 Ndipo msonkhano wonse unatumiza mau kwa ana a Benjamini okhala m'thanthwe la Rimoni, nawalalikira mtendere.

14 Nakwera Abenjamini nthawi ija, ndipo anawapatsa akazi amene anawasunga amoyo mwa akazi a Yabesi-gileadi; koma sanawafikira.

15 Ndipo anthu anamva cifundo pa Benjamini, pakuti Yehova adang'amba mapfuko a Israyeli.

16 Pamenepo akuru a msonkhano anati, Tidzatani, kuwafunira akazi otsalawo, popeza akazi anatha psiti m'Benjamini?

17 Nati iwo, Pakhale colowa ca iwo opulumuka a Benjamini, lingafafanizidwe pfuko m'Israyeli.

18 Koma sitikhoza ife kuwapatsa ana athu akazi akhale akazi ao; pakuti ana a Israyeli adalumbira ndi kuti, Atembereredwe wakupatsa Abenjamini mkazi.

19 Natiiwo, Taonani, pali madyerero a Yehova caka ndi caka ku Silo, ndiko kumpoto kwa Beteli, kum'mawa kwa mseu wokwera kucokera ku Beteli kumka ku Sekemu, ndi kumwela kwa Lebona.

20 Ndipo analamulira ana a Benjamini ndi kuti, Mukani, mulalire m'minda yamphesa;

21 nimuyang'ane, ndipo taonani, ataturuka ana akazi a Silo kubvinabvina, pamenepo muturuke m'minda yamphesa ndi kudzigwirira yense mkazi wace mwa ana akazi a Silo, ndi kumuka naye ku dziko la Benjamini.

22 Ndipo kudzali, akatifikira atate ao kapena alongo ao kunena nafe mlandu, tidzanena nao, Mutipatse awa, pakuti sitinawatengera yense mkazi wace kunkhondo; pakuti inunso simunawaninkha awa; mukadatero mukadaparamula tsopano.

23 Nacita cotere ana a Benjamini, nadzitengera akazi monga mwa kuwerenga kwao, a obvina aja, amene anawatenga mwacifwamba; namuka iwo nabwerera ku colowa cao, namanga midzi, nakhalamo.

24 Ndipo ana a Israyeli anacokako nthawi ija yense kumka ku pfuko lace, ndi banja lace, naturukako yense kumka ku colowa cace.

25 Panalibe mfumu m'Israyeli masiku aja; a yense anacita comkomera pamaso pace.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21