Oweruza 6 BL92

Midyani agonjetsa Aisrayeli

1 Koma ana a Israyeli anacita coipa pamaso pa Yehova; ndipo Yehova anawapereka m'dzanja la Midyani zaka zisanu ndi ziwiri.

2 Pamene dzanja la Midyani linalaka Israyeli, ana a Israyeli anadzikonzera ming'ang'ala ya m'mapiri, ndi mapanga, ndi malinga cifukwa ca Midyani.

3 Ndipo kunali, akabzala Israyeli, amakwera Amidyani, ndi Amaleki, ndi ana a kum'mawa, inde amawakwerera;

4 nawamangira misasa, namaononga zipatso za m'dziko mpaka ufika ku Gaza, osawasiyira cocirira njala m'Israyeli, ngakhale nkhosa, kapena ng'ombe, kapena buru.

5 Pakuti anakwera nazo zoweta zao ndi mahema ao, analowa ngati dzombe kucuruka kwao; iwowa ndi ngamila zao zomwe nzosawerengeka; ndipo analowa m'dziko kuliononga.

6 Ndipo Israyeli anafoka kwambiri cifukwa ca Midyani; ndipo ana a Israyeli anapfuula kwa Yehova.

7 Ndipo kunali, pamene ana a Israyeli anapfuula kwa Yehova cifukwa ca Midyani,

8 Yehova anatuma munthu mneneri kwa ana a Israyeli, nanena nao, Atero Yehova Mulungu wa Israyeli, Ine ndinakukwezani kucokera m'Aigupto, ndi kukuturutsani m'nyumba ya ukapolo;

9 ndipo ndinakulanditsani m'dzanja la Aaigupto, ndi m'dzanja la onse akupsinja inu, ndi kuwaingitsa pamaso panu, ndi kukupatsani dziko lao;

10 ndipo ndinati kwa inu, Ine ndine Yehova Mulungu wanu; musamaopa milungu ya Aamori amene mukhala m'dziko lao; koma simunamvera mau anga.

Mngelowa Mulungu amdzera Gideoni

11 Pamenepo anadza mthenga wa Yehova, nakhala patsinde pa thundu wokhala m'Ofira, wa Yoasi M-abieziri; ndi mwana wace Gideoni analikuomba tirigu m'mopondera mphesa, awabisire Amidyani.

12 Ndipo mthenga wa Yehova anamuonekera, nati kwa iye, Yehova ali nawe, ngwazi iwe, wamphamvu iwe.

13 Ndipo Gideoni ananena naye, Mbuye wanga, ngati Yehova ali nafe catigwera ife bwanji conseci? ndipo ziti kuti zodabwiza zace zonse zimene makolo athu anatiwerengera, ndi kuti, Sanatikweza kodi Yehova kucokera m'Aigupto? Koma tsopano Yehova watitaya natipereka m'dzanja la Midyani.

14 Pamenepo Yehova anamtembenukira, nati, Muka nayo mphamvu yako iyi, nupulumutse Israyeli m'dzanja la Midyani, Sindinakutuma ndi Ine kodi?

15 Ndipo anati kwa iye, Ha! Mbuye, ndidzapulumutsa Israyeli ndi ciani? Taonani, banja langa liri loluluka m'Manase, ndipo ine ndine wamng'ono m'nyumba ya atate wanga.

16 Ndipo Yehova ananena naye, Popeza Ine ndidzakhala nawe udzakantha Amidyani ngati munthu mmodzi.

17 Ndipo anati kwa iye, Ngati mundikomera mtima mundionetse cizindikilo tsopano cakuti ndi Inu wakunena nane.

18 Musacoke pano, ndikupemphani, mpaka ndikudzerani ndi kuturutsa copereka canga ndi kuciika pamaso panu. Ndipo anati, Ndidzalinda mpaka ubwera.

19 Ndipo Gideoni analowa, nakonza kambuzi ndi mikate yopanda cotupitsa ya muyeso wa ufa; nyamayi anaiika m'licero, ndi msuzi anauthira mumbale, naturuka nazo kwa iye ali patsinde pa thundu, nazipereka.

20 Koma mthenga wa Mulungu ananena naye, Tenga nyamayi ndi mikate yopanda cotupitsa ndi kuziika pathanthwe pano ndi kutsanula msuzi. Ndipo anatero.

21 Pamenepo mthenga wa Yehova anatambasula nsonga ya ndodo inali m'dzanja lace, nakhudza nyamayi ndi mikate yopanda cotupitsa; ndipo unaturuka moto m'thanthwe nunyeketsa nyama ndi mikate yopanda cotupitsa; ndi mthenga wa Yehova anakanganuka pamaso pace.

22 Pamenepo Gideoni anaona kuti ndiye mthenga wa Yehova, nati Gideoni, Tsoka ine, Yehova Mulungu! popeza ndaona mthenga wa Yehova maso ndi maso.

23 Ndipo Yehova anati kwa iye, Mtendere ukhale ndi iwe, usaope, sudzafa.

24 Pamenepo Gideoni anammangira Yehova guwa la nsembe pomwepo; nalicha Yehova-ndiyemtendere; likali m'Ofira wa Abieziri ndi pano pomwe.

Gideoni agamula guwa la nsembe la Baala

25 Ndipo kunali, usiku womwe uja Yehova ananena naye, Tenga ng'ombe ya atate wako, ndiyo ng'ombe yaciwiri ya zaka zisanu ndi ziwiri, nugamule guwa la nsembe la Baala ndilo la atate wako, nulikhe cifanizo ciri pomwepo;

26 numangire Yehova Mulungu wako guwa la nsembe pamwamba pa lingali, monga kuyenera; nutenge ng'ombe yaciwiriyo, nufukize nsembe yopsereza; nkhuni zace uyese cifanizo walikhaco.

27 Pamenepo Gideoni anatenga amuna khumi mwa anyamata ace, nacita monga Yehova adanena naye; ndipo kunali, popeza anaopa a ku nyumba ya atate wace, ndi amuna a ku mudziwo, sanacicita msana, koma usiku.

28 Ndipo pakuuka mamawa amuna a ku mudziwo, taonani, guwa la nsembe la Baala litagamuka, ndi cifanizo cinali pomwepo citalikhidwa ndi ng'ombe yaciwiri yoperekedwa pa guwa la nsembe adalimanga.

29 Nanenana wina ndi mnzace, Wacita ici ndani? Ndipo atafunafuna nafunsafunsa, anati, Gideoni, mwana wa Yoasi wacita ici.

30 Pamenepo amuna a ku mudziwo anati kwa Yoasi, Umturutse mwana wako kuti afe; pakuti anagamula guwa la nsembe la Baala, pakutinso analikha cifanizo cinali pomwepo.

31 Koma Yoasi anati kwa onse akumuimirira, Kodi inu mumnenera Baala mlandu? Kapena kodi mudzampulumutsa iye? iye amene amnenera mlandu aphedwe kukali m'mawa; akakhala mulungu adzinenere yekha mlandu, popeza wina wamgamulira guwa lace la nsembe.

32 Cifukwa cace anamucha tsiku lija Yerubaala, ndi kuti, Amnenece mlandu Baala popeza anamgamulira guwa lace la nsembe.

33 Pamenepo Amidyani onse ndi Aamaleki ndi ana a kum'mawa anasonkhana pamodzi naoloka, namanga misasa m'cigwa ca Yezreeli.

34 Koma mzimu wa Yehova unabvana Gideoni; naomba lipenga iye, ndi a banja la Abieziri analalikidwa kumtsata iye.

35 Ndipo anatuma mithenga kwa Manase konse; ndi iwonso analalikidwa kumtsata iye; natuma mithenga kwa Aseri, ndi kwa Zebuloni, ndi kwa Nafitali; iwo nadzakomana nao.

36 Ndipo Gideoni anati kwa Mulungu, Mukadzapulumutsa Israyeli ndi dzanjalanga monga mwanena,

37 taonani, ndidzaika cikopa ca ubweya popunthira tirigu; pakakhala mame pacikopa pokha, ndi panthaka ponse pouma, pamenepo ndidzadziwa kuti mudzapulumutsa Israyeli ndi dzanja langa monga mwanena.

38 Ndipo kunatero; pakuti anauka mamawa, nafinya cikopaco, nakamula mame a pacikopa, madzi ace odzala mbale.

39 Ndipo Gideoni ananena ndi Mulungu, Mkwiyo wanu usandiyakire, ndinene kamodzi kokha: ndikuyeseni kamodzi kokha ndi cikopa; paume pacikopa pokha, ndi panthaka ponse pakhale mame.

40 Ndipo Mulungu anatero usiku uja; pakuti panauma pacikopa pokha, ndi panthaka ponse panali mame.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21