Oweruza 2 BL92

Mngelo wa Mulungu adzudzula Aisrayeli

1 Ndipo mthenga wa Yehova anakwera kucokera ku Giligala kumka ku Bokimu. Ndipo anati, Ndinakukweretsani kucokera ku Aigupto, ndi kulowetsa inu m'dziko limene ndinalumbirira makolo anu; ndipo ndinati, Sindidzathyola cipangano canga nanu ku nthawi yonse;

2 ndipo inu, musamacita pangano ndi nzika za m'dziko ili; muzigamula maguwa ao a nsembe. Koma simunamvera mau anga; mwacicita ici cifukwa ninji?

3 Cifukwa cacenso ndinati, Sindidzawapitikitsa kuwacotsa pamaso panu; koma adzakhala ngati minga m'nthiti zanu, ndi milungu yao idzakhalira inu msampha.

4 Ndipo kunali, pamene mthenga wa Yehova ananena mau awa kwa ana onse a Israyeli, anthuwo anakweza mau ao, nalira misozi.

5 Potero analicha dzina la malowo Bokimu: namphera Yehova nsembe pomwepo.

Aisrayeli alowerera atamwalira Yoswa

6 Pamene Yoswa atawalola anthu amuke, ana a Israyeli anamuka, yense ku colowa cace, dziko likhale lao lao.

7 Ndipo anthuwo anatumikira Yehova masiku onse a Yoswa ndi masiku onse a akulu akulu otsala atafa Yoswa, amene adaona nchito yaikuru yonse ya Yehova anaicitira Israyeli.

8 Ndipo Yoswa mwana wa Nuni, mtumiki wa Yehova anafa wa zaka zace zana ndi khumi.

9 Ndipo anamuika m'malire a colowa cace m'Timinatiheresi, ku mapiri a Efraimu, kumpoto kwa phiri la Gaasi.

10 Ndiponso mbadwo uwu wonse unasonkhanidwa kuikidwa kwa makolo ao; nuuka mbadwo wina pambuyo pao; wosadziwa Yehova kapena nchitoyi adaicitira Israyeli,

11 Ndipo ana a Israyeli anacita coipa pamaso pa Yehova, natumikira Abaala;

12 nasiya Yehova Mulungu wa makolo ao, amene adawaturutsa m'dziko la Aigupto, natsata milungu yina, milungu ya mitundu ya anthu okhala pozungulira pao, naigwadira; nautsa mkwiyo wa Yehova.

13 Ndipo anasiya Yehova, natumikira Baala ndi Asitaroti.

14 Pamenepo mkwiyo wa Yehova unayakira Israyeli, ndipo anawapereka m'manja a ofunkha kuti awafunkhe; nawagulitsa m'dzanja la adani ao akuwazungulira osakhozanso iwowo kuima pamaso pa adani ao.

15 Kuli konse anaturuka, dzanja la Yehova linawakhalira moipa, monga Yehova adanena, ndi monga Yehova adawalumbirira; nasautsika kwambiri iwowa.

16 Ndipo Yehova anautsa oweruza, amene anawapulumutsa m'dzanja la iwo akuwafunkha.

17 Koma sanamvera angakhale oweruza ao, pakuti anamuka kupembedza milungu yina, naigwadira; anapambuka msanga m'njira yoyendamo makolo ao, pomvera malamulo a Yehova; sanatero iwowa.

18 Ndipo pamene Yehova anawaukitsira oweruza, Yehova anakhala naye woweruzayo, nawapulumutsa m'dzanja la adani ao masiku onse a woweruzayo; pakuti Yehova anagwidwa cisoni pa kubuula kwao cifukwa ca iwo akuwapsinja ndi kuwatsendereza.

19 Koma kunali atafa woweruzayo anabwerera m'mbuyo, naposa makolo ao ndi kucita moipitsa, ndi kutsata milungu yina kuitumikira ndi kuigwadira, sanaleka kanthu ka macitidwe ao kapena ka njira yao yacheni.

20 Ndipo mkwiyo wa Yehova unayakira Israyeli; nati Iye, Popezamtundu uwu unalakwira cipangano canga cunene ndinalamulira makolo ao, osamvera mau ansa;

21 lnenso sindionjeza kuingitsa pamaso pao a mitundu yina imene Yoswa adaisiya pakufa iyeyu;

22 kuti ndiyese nayo Israyeli ngati adzasunga njira ya Yehova kuyendamo monga anaisunga makolo ao, kapena iai.

23 Motero Yehova analeka mitundu iyi osaiingitsa msanga, ndipo sadaipereka m'dzanja la yoswa.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21