1 Pamenepo anaturuka ana onse a Israyeli, nuunjikana msonkhano kwa Yehova ku Mizipa ngati munthu mmodzi, kuyambira ku Dani mpaka Beereseba ndi dziko la Gileadi lomwe.
2 Ndipo akuru a anthu onse a mapfuko onse a Israyeli anadziimika mu msonkhano wa anthu a Mulungu, anthu oyenda pansi zikwi mazana anai akusolola lupanga,
3 Ndipo ana a Benjamini anamva kuti ana a Israyeli adakwera kumka ku Mizipa, Nati ana a Israyeli, Nenani, coipa ici cinacitika bwanji?
4 Ndipo Mlevi, mwamuna wa mkazi anaphedwayo, anayankha nati, Ndinadza ine ku Gibeya wa Benjamini, ine ndi mkazi wanga wamng'ono, kugonako.
5 Nandiukira eni ace a Gibeya, nandizingira nyumba usiku; nafuna kundipha ine, namcitira coipa mkazi wanga wamng'ono, nafa iye,
6 Pamenepo ndinagwira mkazi wanga wamng'ono ndi kumgawa ndi kumtumiza m'dziko lonse la colowa ca Israyeli, pakuti anacita cocititsa manyazi ndi copusa m'lsrayeli.
7 Taonani, inu nonse, ndinu ana a Israyeli, mudzinenere mau ndi kudzipangira nokha kuno.
8 Ndipo anthu onse anauka ngati munthu mmodzi, ndi kuti, Palibe mmodzi wa ife adzamuka kuhema kwace, kapena kupambukira nyumba yace,
9 koma tsopano ici ndico tidzacitira Gibeya: tidzaukwerera ndi kulota maere.
10 Ndipo tidzatapa amuna khumi limodzi pa zana limodzi, mwa mapfuko onse a Israyeli; ndi zana limodzi pa zikwi cimodzi, ndi cikwi cimodzi pa zikwi khumi kutengera anthu kamba; kuti pakufika ku Gibeya wa Benjamini, aucitire monga mwa copusa conse unacita m'Israyeli.
11 Potero amuna onse a Israyeli anasonkhanira mudziwo, olunzika ngati munthu mmodzi.
12 Ndipo mapfuko a Israyeli anatuma anthu mwa pfuko lonse la Benjamini, ndi kuti, Coipa canji ici cinacitika mwa inu?
13 Ndipo tsopano perekani amunawo otama zopanda pace, okhala m'Gibeya, kuti tiwaphe, ndi kucotsera Israyeli coipaci. Koma Benjamini sanafuna kumvera mau a abale ao, ana a Israyeli.
14 Ndipo ana a Benjamini anasonkhana kucokera ku midzi kumka ku Gibeya, kuti aturuke kulimbana ndi ana a Israyeli.
15 Ndipo anawerenga ana a Benjamini a m'midzi tsiku lija amuna zikwi makumi awiri mphambu zisanu ndi cimodzi akusolola lupanga; osawerenga okhala m'Gibeya, ndiwo amuna osankhika mazana asanu ndi awiri.
16 Mwa anthu awa onse munali amuna osankhika mazana asanu ndi awiri amanzere, yense wa iwo amaponya mwala mwa maluli osaphonya.
17 Ndipo anawerenga amuna a Israyeli, osati Benjamini, amuna zikwi mazana anai osolola lupanga, anthu a nkhondo okha okha.
18 Nauka ana a Israyeli, nakwera kumka ku Beteli, nafunsira kwa Mulungu, nati, Ayambe ndani kutikwerera pa ana a Benjamini? Ndipo Yehova anati, Ayambe ndi Yuda.
19 Nauka ana a Israyeli m'mawa, naumangira Gibeya misasa.
20 Ndipo amuna a Israyeli anaturuka kulimbana ndi Benjamini; ndi amuna a Israyeli anawandandalikira nkhondo ku Gibeya.
21 Pamenepo ana a Benjamini anaturuka m'Gibeya, naononga a Israyeli tsiku lija zikwi makumi awiri mphambu ziwiri, kuwagoneka pansi,
22 Koma anthu, ndiwo amuna a Israyeli, anadzilimbitsa nanikanso nkhondo kumene anandandalika tsiku loyambalo.
23 Ndipo ana a Israyeli anakwera nalira misozi pamaso pa Yehova mpaka madzulo; nafunsira kwa Yehova ndi kuti, Ndiyandikizenso kodi kulimbana nkhondo ndi ana a Benjamini mbale wanga? Ndipo Yehova anati, Mumkwerere.
24 Potero ana a Israyeli anayandikira ana a Benjamini m'mawa mwace.
25 Ndipo Benjamini anawaturukira ku Gibeya m'mawa mwace, naononganso a ana a Israyeli amuna zikwi khumi ndi zisanu ndi zitatu kuwagoneka pansi; ndiwo onse osolola lupanga.
26 Pamenepo ana onse a Israyeli ndi anthu onse anakwera nafika ku Beteli, nalira misozi, nakhala pansi pomwepo pamaso pa Yehova, nasala cakudya tsiku lomwelo mpaka madzulo; napereka nsembe zopsereza ndi nsembe zoyamika pamaso pa Yehova.
27 Ndipo ana a Israyeli anafunsira kwa Yehova; pakuti likasa la cipangano la Mulungu linakhala komweko masiku aja,
28 namaima ku likasalo Pinehasi mwana wa Eleazare mwana wa Aroni, masiku aja; nati, Kodi nditurukenso kulimbana nkhondo ndi ana a Benjamini mbale wanga, kapena ndileke Ndipo Yehova anati, Kwerani, pakuti mawa ndidzampereka m'dzanja lako.
29 Ndipo Israyeli anaika olalira Gibeya pozungulira pace.
30 Ndipo ana a Israyeli anakwerera ana a Benjamini tsiku lacitatu, na nika pa Gibeya monga nthawi zina.
31 Naturuka ana a Benjamini kukomana ndi anthuwo, nakokedwa kutali ndi mudzi, nayamba kuwakantha ndi kuwapha anthu amuna a Israyeli, ngati makumi atatu monga nthawi zina, m'makwalala, limodzi la awo lokwera kumka ku Beteli, ndi lina ku Gibeya kuthengo.
32 Ndipo ana a Benjamini anati, Tawakantha pamaso pathu monga poyamba paja. Koma ana a Israyeli anati, Tithawe, tiwakokere kutari ndi mudzi kumakwalala.
33 Nauka amuna onse a Israyeli m'malo ao nanika ku Baalatamari; naturuka Aisrayeli olalira aja m'malo mwao, m'Maare-geba.
34 Ndipo anadza pandunji pa Gibeya amuna osankhika m'Israyeli monse zikwi khumi, nikula nkhondo; koma sanadziwa kuti coipa ciri pafupi kuwakhudza.
35 Ndipo Yehova anakantha Benjamini pamaso pa Israyeli; ndi ana a Israyeli anawaononga a Benjamini tsiku lija amuna zikwi makumi awiri ndi zisanu, kudza zana limodzi; awa onse ndiwo akusolola lupanga.
36 Ndipo ana a Benjamini anaona kuti takanthidwa; popeza amuna a Israyeli anawapatsa Abenjamini malo, pakuti anatama olalira amene anawaikiratu pa Gibeya.
37 Nafulumira olalirawo nathamangira Gibeya, nabalalika olalirawo, nakantha mudzi wonse ndi lupanga lakuthwa.
38 Koma kunali cizindikilo coikika pakati pa amuna a Israyeli ndi olalirawo, ndico cakuti afukitse mtambo wa utsi kumudzi.
39 Ndi nkhondo ya Israyeli inathawa, ndipo Benjamini anayamba kuwakantha ndi kuwagwaza amuna a Israyeli, ngati amuna makumi atatu, pakuti anati, Ndithu Tawakantha konse pamaso pathu, monga ku nkhondo yoyambayo.
40 Koma pamene mtambo unayamba kukwera m'mudzi ngati utsi uti tolo, Abenjamini anaceuka, ndipo taonani, pamodzi ponse panafuka utsi kumwamba.
41 Natembenuka amuna a Israyeli; nadabwa amuna a Benjamini; popeza anaona kuti cidawagwera coipa.
42 Nabwerera iwo pamaso pa amuna a Israyeli kumka njira ya cipululu; koma nkhondo inawaloodetsa; ndi aja oturuka m'mudzi anawaononga pakati pao.
43 Anawazinga Abenjamini, anawapitikitsa, nawapondereza pampumulo mpaka pandunji pa Gibeya, koturukira dzuwa.
44 Ndipo adagwa a Benjamini amuna zikwi khumi ndi zisanu ndi zitatu; iwo onse ndiwo ngwazi.
45 Natembenuka iwo, nathawira kucipululu ku thanthwe la Rimoni; koma anawakunkha m'makwalala amuna zikwi zisanu; nawalondetsa ku Gidomu, nakantha a iwowa amuna zikwi ziwiri.
46 Potero onse amene adagwa a Benjamini tsiku lija, ndiwo amuna zikwi makumi awiri mphambu zisanu, akusolola lupanga; iwo onse ndiwo ngwazi.
47 Koma amuna mazana asanu ndi limodzi anabwerera nathawira kucipululu, ku thanthwe la Rimoni, nakhala m'thanthwe la Rimoni miyezi inai.
48 Ndipo amuna a Israyeli anabwereranso kwa ana a Benjamini, nawakantha ndi lupanga lakuthwa a m'mudzi wonse, ndi zoweta, ndi zonse adazipeza; anatenthanso midzi yonse anaipeza.