Oweruza 17 BL92

Mika ndi fano lace

1 Ndipo ku mapiri a Efraimu kunali munthu dzina lace ndiye Mika.

2 Ndipo iye anati kwa amai wace, Ndarama zija mazana khumi ndi limodzi anakuberani zimene munatembererapo, ndi kunenanso m'makutu mwanga, taonani ndaramazo ndiri nazo, ndinazitenga ndine. Pamenepo amai wace anati, Yehova adalitse mwana wanga.

3 Nabwezera amace ndarama zija mazana khumi ndi limodzi; nati amai wace, Kupatula ndapatulira Yehova ndaramazo zicoke ku dzanja langa, zimuke kwa mwana wanga, kupanga nazo dikupempha fano losema ndi fane loyenga; m'mwemo ndikubwezera izi.

4 Ndipo pamene anambwezera mai wace ndaramazo, mai wace anatapako ndarama mazana awiri, nazipereka kwa woyenga, ndiye anazipanga fane losema ndi fano loyenga; ndipo linakhala m'nyumba ya Mika.

5 Koma munthuyu Mika anali nayo nyumba ya milungu, napanga cobvala ca wansembe, ndi timafano, namninkha zansembe mwana wace wina wamwamuna, amene anakhala wansembe wace.

6 Masikuwa panalibe mfumu m'Israyeli, yense anacita comuyenera m'maso mwace.

7 Ndipo panali mnyamata wa ku Betelehemu-Yuda wa banja la Yuda, ndiye Mlevi, nagonera iye komweko.

8 Adacokera munthuyo m'mudzi m'Betelehemu-Yuda, kugonera pali ponse akapeza pokhala; ndi pa ulendo wace anafika ku mapiri a Efraimu, ku nyumba ya Mika.

9 Ndipo Mika ananena naye, Ufumira kuti? Nati kwa iye, Ndine Mlevi wa ku Betelehemu-Yuda, ndirikumuka kugonera kumene ndikapeza pokhala.

10 Nanena naye Mika, Khalitsa nane, nukhale atate wanga, ndi wansembe wanga, ndipo ndidzakupatsa ndarama khumi pacaka, ndi cobvala cofikira, ndi zakudya zako. Nalowa Mleviyo.

11 Ndi Mleviyo anabvomera kukhalitsa ndi munthuyo; ndi mnyamatayo anamkhalira ngati mmodzi wa ana ace.

12 Ndipo Mika anamninkha zansembe Mleviyo, ndi mnyamatayo anakhala wansembe wace, nakhala m'nyumba ya Mika.

13 Nati Mika, Tsopano ndidziwa kuti Yehova adzandicitira cokoma, popeza ndiri naye Mlevi akhale wansembe wanga.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21