2 Ndipo anaweruza Israyeli zaka makumi awiri ndi zitatu, nafa, naikidwa m'Samiri.
3 Atafa iye, anauka Yairi Mgileadi, naweruza Israyeli zaka makumi awiri mphambu ziwiri.
4 Ndipo anali nao ana amuna makumi atatu okwera pa ana a aburu makumi atatu, iwo ndipo anali nayo midzi makumi atatu, ochedwa midzi ya Yairi, mpaka lero lino, ndiyo m'dziko la Gileadi.
5 Nafa Yairi, naikidwa m'Kamoni.
6 Ndipo ana Israyeli a anaonjeza kucita coipa pamaso pa Yehova, natumikira Abaala, ndi Aastaroti, ndi milungu ya Aramu, ndi milungu ya Sidoni, ndi milungu ya Moabu, ndi milungu ya ana a Amoni, ndi milungu ya Afilisti; ndipo anamleka Yehova osamtumikira.
7 Pamenepo mkwiyo wa Yehova unayakira Israyeli, nawagulitsa m'dzanja la Aftlisti, ndi m'dzanja la ana a Amoni.
8 Ndipo anaphwanya napsinja ana a Israyeli caka ciija, natero ndi ana onse a Israyeli okhala tsidya lija la Yordano m'dziko la Aamori, ndilo Gileadi, zaka khumi ndi zisanu ndi zitatu.