7 Pamenepo mkwiyo wa Yehova unayakira Israyeli, nawagulitsa m'dzanja la Aftlisti, ndi m'dzanja la ana a Amoni.
8 Ndipo anaphwanya napsinja ana a Israyeli caka ciija, natero ndi ana onse a Israyeli okhala tsidya lija la Yordano m'dziko la Aamori, ndilo Gileadi, zaka khumi ndi zisanu ndi zitatu.
9 Ndipo ana a Amoni anaoloka Yordano kuthiranso nkhondo Yuda ndi Benjamini, ndi nyumba ya Efraimu; napsinjika kwambiri Israyeli.
10 Ndipo ana a Israyeli anapfuula kwa Yehova ndi kuti, Takucimwirani, popeza tasiya Mulungu wathu ndi kutumikira Abaala.
11 Ndipo Yehova anati kwa ana a Israyeli, Kodi sindinakupulumutsani kwa Aaigupto ndi kwa Aamori, ndi kwa ana a Amoni, ndi kwa Aftlisti?
12 Asidoni omwe, ndi Aamaleki, ndi Amidyani anakupsinjani. Pamenepo munapfuula kwa Ine, ndipo ndinakupulumutsani m'dzanja lao.
13 Koma mwandisiya Ine ndi kutumikira milungu yina, cifukwa cace sindikupulumutsaninso.