1 Ndipo ana a Israyeli anaonjeza kucita coipa pamaso pa Yehova; nawapereka Yehova m'dzanja la Afilisti zaka makumi anai.
2 Ndipo panali munthu wina wa Zora wa banja la Adani, dzina lace ndiye Manowa; ndi mkazi wace analibe mwana, sanabala.
3 Ndipo mthenga wa Yehova anamuonekera mkaziyo nanena naye, Taona tsopano, ulibe mwana, wosabala iwe; koma udzaima ndi kubala mwana wamwamuna.
4 Cifukwa cace udzisamalire, usamwe vinyo kapena coledzeretsa, nusadye cinthu ciri conse codetsa;