1 Ndipo ana a Israyeli anaonjeza kucita coipa pamaso pa Yehova; nawapereka Yehova m'dzanja la Afilisti zaka makumi anai.
2 Ndipo panali munthu wina wa Zora wa banja la Adani, dzina lace ndiye Manowa; ndi mkazi wace analibe mwana, sanabala.
3 Ndipo mthenga wa Yehova anamuonekera mkaziyo nanena naye, Taona tsopano, ulibe mwana, wosabala iwe; koma udzaima ndi kubala mwana wamwamuna.
4 Cifukwa cace udzisamalire, usamwe vinyo kapena coledzeretsa, nusadye cinthu ciri conse codetsa;
5 pakuti taona, udzaima, nudzabala mwana wamwamuna; pamutu pace sipadzafika lumo; pakuti mwanayo adzakhalira kwa Mulungu Mnaziri cibadwire; nadzayamba iye kupulumutsa Israyeli m'dzanja la Afilisti.
6 Pamenepo anadza mkaziyo, nanena ndi mwamuna wace ndi kuti, Wandidzera munthu wa Mulungu; maonekedwe ace ndiwo ngati maonekedwe a mthenga wa Mulungu oopsa ndithu; ndipo sindinamfunsa uko acokera kapena sanandiuzanso dzina lace;