10 cifukwa cakuopa cizunzo cace, nanena, Tsoka, tsoka, mudzi waukuruwo, Babulo, mudzi wolimba! pakuti m'ora limodzi cafika ciweruziro canu.
11 Ndipo ocita malonda a m'dziko adzalira nadzaucitira cifundo, popeza palibe munthu agulanso malonda ao;
12 malonda a golidi, ndi a siliva, ndi a mwala wa mtengo wace, ndi a ngale, ndi a nsaru yabafuta, ndi a cibakuwa, ndi a yonyezimira, ndi a mlangali; ndi mitengo yonse ya pfungo lokoma, ndi cotengera ciri conse ca minyanga ya njobvu, ndi cotengera ciri conse camtengo wa mtengo wace wapatali, ndi camkuwa ndi cacitsulo, ndi cansangalabwi;
13 ndi kinamomo ndi amomo, ndi zofukiza, ndi zodzola, ndi libano, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi ufa wosalala, ndi tirigu, ndi ng'ombe, ndi nkhosa; ndi malonda a akavalo, ndi a magareta, ndi a anthu ndi a miyoyo ya anthu.
14 Ndipo zokhumbitsa moyo wako zidakucokera; ndipo zonse zolongosoka, ndi zokometsetsa zakutayikira, ndipo izi sudzazipezanso konse.
15 Otsatsa izi, olemezedwa nao, adzaima patali cifukwa ca kuopa cizunzo cace, nadzalira, ndi kucita cifundo;
16 nadzanena, Tsoka, tsoka, mudzi waukuru wobvala bafuta ndi cibakuwa, ndi mlangali, wodzikometsera ndi golidi, ndi mwala wa mtengo wace, ndi ngale!