1 Zitatha izi ndinamva ngati a mau akuru khamu lalikuru m'Mwamba, liri kunena, Aleluya; cipulumutso, ndi ulemerero, ndi mphamvu, nza Mulungu wathu;
2 pakuti maweruzo ace ali oona ndi olungama; ndipo anaweruza mkazi wacigololo wamkuru, amene anaipsa dziko ndi cigololo cace, ndipo anabwezera cilango mwazi wa akapolo ace pa dzanja lace la mkaziyo.
3 Ndipo anatinso, Aleluya. Ndipo utsi wace ukwera ku nthawi za nthawi.
4 Ndipo anagwa pansi akuluwo makumi awiri mphambu anai ndi zamoyo zinai, ndipo zinalambira Mulungu wakukhala pa mpando wacifumu, nizinena, Amen; Aleluya.
5 Ndipo mau anacokera ku mpando wacifumu, ndi kunena, Lemekezani Mulungu wathu akapolo ace onse, akumuopa iye, ang'ono ndi akuru.
6 Ndipo ndinamva ngati mau a khamu lalikuru, ngati mkokomo wa madzi ambiri, ngati mau a mabingu olimba, nizinena, Aleluya; pakuti acita ufumu Ambuye Mulungu wathu, Wamphamvuyonse.