1 Kwa mngelo wa Mpingo wa ku Efeso lemba;Izi azinena iye amene agwira nyenyezi zisanu ndi ziwiri m'dzanja lace lamanja, iye amene ayenda pakati pa zoikapo nyali zisanu ndi ziwiri zagolidi:
2 Ndidziwa nchito zako, ndi cilemetso cako ndi cipiriro cako, ndi kuti sukhoza kulola oipa, ndipo unayesa iwo amene adzicha okha atumwi, osakhala atumwi, nuwapeza onama;
3 ndipo uli naco cipiriro, ndipo walola cifukwa ca dzina langa, wosalema.
4 Koma ndiri nako kanthu kotsutsana ndi iwe, kuti unataya cikondi cako coyamba.
5 Potero kumbukila kumene wagwerako, nulape, nucite nchito zoyamba; koma ngari sutero, ndidzadza kwa iwe, ndipo ndidzatunsa coikapo nyali cako, kucicotsa pamalo pace, ngati sulapa.
6 Koma ici uli naco, kuti udana nazo nchito za Anikalai, zimene Inenso ndidana nazo.
7 Iye wokhala nalo khutu amve cimene Mzimu anena kwa Mipingo, K wa iye amene alakika ndidzampatsa kudya za ku mtengo wa moyo umene uli m'Paradaiso wa Mulungu.