12 Ndipo ndinaona akufa, akuru ndi ang'ono alinkuima ku mpando wacifumu; ndipo mabuku anatsegulidwa; ndipo buku lina Iinatsegulidwa, ndilo la moyo; ndipo akufa anaweruzidwa mwa zolembedwa m'mabuku, monga mwa nchito zao.
13 Ndipo nyanja inapereka akufawo anali momwemo, ndipo imfa ndi Hade zinapereka akufawo anali m'menemo; ndipo anaweruzidwa yense monga mwa nchito zace,
14 Ndipo imfa ndi Hade zinaponyedwa m'nyanja yamoto. Iyo ndiyo imfa yaciwiri, ndiyo nyanja yamoto.
15 Ndipo ngati munthu sanapezedwa wolembedwa m'buku la moyo, anaponyedwa m'nyanja yamoto.