16 Ndipo mzinda ukhala wampwamphwa; utali wace ulingana ndi kupingasa kwace: ndipo anayesa mzinda ndi bangolo, mastadiya zikwi khumi ndi ziwiri; utali wace, ndi kupingasa kwace, ndi kutalika kwace zilingana.
17 Ndipo anayesa linga lace, mikono zana mphambu makumi anai kudza zinai, muyeso wa munthu, ndiye mngelo.
18 Ndipo mirimo ya linga lace ndi yaspi; ndipo mzindawo ngwagolidi woyengeka, wofanana ndi mandala oyera.
19 Maziko a linga la mzinda anakometsedwa ndi miyala ya mtengo, ya mitundu mitundu; mazikooyamba, ndi yaspi; aciwiri, ndi safiro; acitatu, ndi kalikedo; acinai, ndi smaragido;
20 acisanu, ndi sardoau; acisanu ndi cimodzi, ndi sardiyo; acisanu ndi ciwiri, ndi krusolito; acisanu ndi citatu, ndi berulo; acisanu ndi cinai, ndi topaziyo; akhumi, ndi krusoprazo; akhumi ndt cimodzi, ndi huakinto; akhumi ndi ciwiri, ndi ametusto.
21 Ndipo zitseko khumi ndi ziwiri ndizo ngale khumi ndi ziwiri; citseko ciri conse pa cokha ca ngale imodzi. Ndipo khwalala la mzinda ma golidi woyengeka, ngati mandala openyekera.
22 Ndipo siridinaona Kacisi momwemo; pakuti Ambuye Mulungu Wamphamvuyonse, ndi Mwanawankhosa ndiwo Kacisi wace.