6 Ndipo anati kwa ine, Mau awa ali okhulupirika ndi oona; ndipo Ambuye, Mulungu wa mizimu ya aneneri, anatuma mngelo wace kukaonetsera akapolo ace zimene ziyenera kucitika msanga.
7 Ndipo taonani, ndidza msanga. Wodala iye amene asunga mau a cinenero ca buku ili.
8 Ndipo ine Yohane ndine wakumva ndi wakupenya izi. Ndipo pamene ndinamva ndi kupenya, ndinagwa pansi kulambira pa mapazi a mngelo wakundionetsa izo.
9 Ndipo ananena kwa ine, Tapenya, usacite; ndine kapolo mnzako, ndi mnzao wa abale ako aneneri, ndi wa iwo akusunga mau a buku ili; lambira Mulungu.
10 Ndipo ananena ndi ine, Usasindikiza cizindikilo mau a cinenero ca buku ili; pakuti nthawi yayandikira.
11 Iye wakukhala wosalungama acitebe zosalungama; ndi munthu wonyansa akhalebe wonyansa; ndi iye wakukhala wolungama acitebe colungama; ndi iye amene ali woyera akhalebe woyeretsedwa.
12 Taonani, ndidza msanga; ndipo mphotho yanga ndiri nayo yakupatsa yense monga mwa nchito yace.