3 Cifukwa cace kumbukila umo unalandira nunamvamo; nusunge nulape. Ukapanda kudikira tsono, ndidzafika ngati mbala, ndipo sudzazindikira nthawi yace ndidzadza pa iwe.
4 Komatu uli nao maina owerengeka m'Sarde, amene sanadetsa zobvala zao; ndipo adzayenda ndi Ine m'zoyera; cifukwa ali oyenera.
5 Iye amene alakika adzambveka motero zobvala zoyera; ndipo sindidzafafaniza ndithu dzina lace m'buku la moyo, ndipo ndidzambvomereza dzina lace pamaso pa Atate wanga, ndi pamaso pa angelo ace.
6 Iye wakukhala nalo khutu amve cimene Mzimu anena kwa Mipingo.
7 Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Filadelfeya lemba;Izi anena iye amene ali Woyera, iye amene ali Woona, iye wakukhala naco cifungulo ca Davide, iye wotsegula, ndipo palibe wina atseka; iye wotseka, ndipo palibe wina atsegula:
8 Ndidziwa nchito zako (taona, ndapatsa pamaso pako khomo lotseguka limene munthu sakhoza kutsekapo), kuti uli nayo mphamvu pang'ono, ndipo unasunga mau anga, osakana dzina langa.
9 Taona, ndikupatsa ena oturuka m'sunagoge wa Satana akudzinenera okha ali Ayuda, osakhala Ayuda, komatu anama; taona, ndidzawadzetsa alambire pa mapazi ako, nazindikire kuti Ine ndakukonda.