7 Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Filadelfeya lemba;Izi anena iye amene ali Woyera, iye amene ali Woona, iye wakukhala naco cifungulo ca Davide, iye wotsegula, ndipo palibe wina atseka; iye wotseka, ndipo palibe wina atsegula:
8 Ndidziwa nchito zako (taona, ndapatsa pamaso pako khomo lotseguka limene munthu sakhoza kutsekapo), kuti uli nayo mphamvu pang'ono, ndipo unasunga mau anga, osakana dzina langa.
9 Taona, ndikupatsa ena oturuka m'sunagoge wa Satana akudzinenera okha ali Ayuda, osakhala Ayuda, komatu anama; taona, ndidzawadzetsa alambire pa mapazi ako, nazindikire kuti Ine ndakukonda.
10 Popeza unasunga mau a cipiriro canga, Inenso ndidzakusunga kukulanditsa mu nthawi ya kuyesedwa, ikudza pa dziko lonse lapansi, kudzayesa iwo akukhala padziko.
11 Ndidza msanga; gwira cimene uli naco, kuti wina angalande korona wako.
12 Iye wakulakika, ndidzamyesa iye mzati wa m'Kacisi wa Mulungu wanga, ndipo kuturuka sadzaturukamonso; ndipo ndidzalemba pa iye dzina la Mulungu wanga, ndi dzina la mzinda wa Mulungu wanga, la Yerusalemu watsopano, wotsika m'Mwamba, kucokera kwa Mulungu wanga; ndi dzina langa latsopano.
13 Iye wakukhala nalo khutu amve cimene Mzimu anena kwa Mipingo.