1 Zitatha izi ndinapenya, ndipo taonani, khomo lotseguka m'Mwamba, ndipo mau oyamba ndinawamva, ngati lipenga Iakulankhuia ndi ine, anati, Kwera kuno, ndipo ndidzakuonetsa zimene ziyenera kucitika m'tsogolomo.
2 Pomwepo ndinakhala mwa Mzimu; ndipo, taonani padaikika mpando wacifumu m'Mwamba ndi pa mpandowo padakhala wina;
3 ndipo maonekedwe a iye wokhalapo anafanana ndi mwaia wa jaspi, ndi sardiyo; ndipo panali utawaleza wozinga mpando wacifumu, maonekedwe ace ngati smaragido.
4 Ndipo pozinga mpando yacifumu mipando yacifumu makumi awiri mphambu inai; ndipo pa mipandoyo padakhala akuru makumi awiri mphambu anai, atabvala zobvala zoyera, ndi pamitu pao akorona agolidi.
5 Ndipo mu mpando wacifumu mudaturuka mphezi ndi mau ndi mabingu. Ndipo panali nyali zisanu ndi ziwiri za mota zoyaka ku mpando wacifumu, ndiyo Mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu;
6 ndipo ku mpandowo, ngati nyanja, yamandala yonga krustalo; ndipopakati pa mpandowo, ndi pozinga mpandowo, zamoyo zinai zodzaia ndi maso kutsogolo indi kumbuyo.