11 Ndipo Iye ananena nao, Kwa inu kwapatsidwa cinsinsi ca Ufumu wa Mulungu; koma kwa iwo ali kunja zonse zicitidwa m'mafanizo;
12 kuti kupenya apenye, koma asazindikire; ndipo kumva amve, koma asadziwitse; kuti pena angatembenuke, ndi kukhululukidwa.
13 Ndipo ananena nao, Simudziwa kodi fanizo ili? mukazindikira bwanji mafanizo onse?
14 Wofesa afesa mau.
15 Ndipo iwo ndiwo a m'mbali mwa njira mofesedwamo mau; ndipo pamene anamva, pomwepo akudza Satana nacotsa mau ofesedwa mwa iwo.
16 Ndipo momwemonso iwo ndiwo amene afesedwa pathanthwe, atamva mau, awalandira pomwepo ndi kusekera;
17 ndipo alibe mizu mwa iwo okha, koma akhala kanthawi; pamenepo pakudza masautso kapena mazunzo cifukwa ca mau, pomwepo akhumudwa.