9 Ndipo ananena, Amene ali nao makutu akumva amve.
10 Ndipo pamene anakhala pa yekha, iwo amene anali pafupi ndi Iye pamodzi ndi khumi ndi awiriwo anamfunsa za mafanizo.
11 Ndipo Iye ananena nao, Kwa inu kwapatsidwa cinsinsi ca Ufumu wa Mulungu; koma kwa iwo ali kunja zonse zicitidwa m'mafanizo;
12 kuti kupenya apenye, koma asazindikire; ndipo kumva amve, koma asadziwitse; kuti pena angatembenuke, ndi kukhululukidwa.
13 Ndipo ananena nao, Simudziwa kodi fanizo ili? mukazindikira bwanji mafanizo onse?
14 Wofesa afesa mau.
15 Ndipo iwo ndiwo a m'mbali mwa njira mofesedwamo mau; ndipo pamene anamva, pomwepo akudza Satana nacotsa mau ofesedwa mwa iwo.