29 Atate wanga, amene anandipatsa izo, ali wamkulu ndi onse; ndipo palibe wina angathe kuzikwatula m'dzanja la Atate.
30 Ine ndi Atate ndife amodzi.
31 Ayuda anatolanso miyala kuti amponye iye.
32 Yesu anayankha iwo, ndakuonetsani inu nchito zabwino zambiri za kwa Atate; cifukwa ca nchito yiti ya izo mundiponya miyala?
33 Ayuda anamyankha iye, Cifukwa ca nchito yabwino sitikuponyani miyala, koma cifukwa ca mwano; ndi kuti Inu, muli munthu, mudziyesera nokha Mulungu,
34 Yesu anayankha iwo, Kodi sikulembedwa m'cilamulo canu, Ndinati Ine, Muli milungu?
35 Ngati anawacha milungu iwo amene mau a Mulungu anawadzera (ndipo colemba sicingathe kutyoka),