6 Fanizo ili Yesu ananena kwa iwo; koma sanazindikira zimene Yesu analikulankhula nao.
7 Cifukwa cace Yesuananenanso nao, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Ine ndine khomo la nkhosa.
8 Onse amene anadza m'tsogolo mwa Ine ali akuba, ndi olanda: koma nkhosa sizinamva iwo.
9 Ine ndine khomo; ngati wina alowa ndi Ine, adzapulu-mutsidwa, nadzalowa, nadzaturuka, nadzapeza busa.
10 Siikudza mbala, koma kuti ikabe, ndi kupha, ndi kuononga, Ndadza Ine kuti akhale ndi moyo, ndi kukhala nao wocuruka.
11 Ine ndine Mbusa Wabwino; mbusa wabwino ataya moyo wace cifukwa ca nkhosa.
12 Wolipidwa amene sakhala mbusa, amene nkhosa siziri zace za yekha, aona mmbulu ulinkudza, nasiya nkhosazo, nathawa; ndipo mmbulu uzikwatula, nuzibalalitsa;