20 Koma panali Ahelene ena mwa iwo akukwera kunka kukalambira paphwando,
21 Ndipo iwo anadza kwa Filipo wa ku Betsaida wa m'Galileya, namfunsa iye, ndi kuti, Mbuye, tifuna kuona Yesu.
22 Filipo anadza nanena kwa Andreya; nadza Andreya ndi Filipo, nanena ndi Yesu.
23 Koma Yesu anayankha iwo, nati, Yafika nthawi, kuti Mwana wa munthu alemekezedwe.
24 Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Ngati mbeu ya tirigu siigwa m'nthaka, nifa, ikhala pa yokha iyo; koma ngati ifa, ibala cipatso cambiri.
25 Iye wokonda moyo wace adzautaya; ndipo wodana ndi moyo wace m'dziko lino lapansi adzausungira ku moyo wosatha.
26 Ngati wina anditumikira Ine, anditsate; ndipo kumene kuli Ine, komwekonso kudzakhala mtumiki wanga, Ngati wina anditumikira Ine, Atate adzamcitira ulemu iyeyu,