29 Cifukwa cace khamu la anthu akuimirirako, ndi kuwamva ananena kuti kwagunda. Ena ananena, Mngelo walankhula ndi iye.
30 Yesu anayankha nati, Mau awa sanafika cifukwa ca Ine, koma ca inu.
31 Tsopano pali kuweruza kwa dziko ili lapansi; mkulu wa dziko ili lapansi adzatayidwa kunja tsopano,
32 Ndipo Ine, m'mene ndikakwezedwa kudziko, ndidzakoka anthu onse kwa Ine ndekha.
33 Koma ananena ici ndi kuzindikiritsa imfa yanji akuti adzafa nayo.
34 Pamenepo khamulo linayankha iye, Tidamva ife m'cilamulo kuti Kristu akhala ku nthawi yonse; ndipo Inu munena bwanji, kuti Mwana wa munthu ayenera kukwezedwa? Mwana wa munthu amene ndani?
35 Pamenepo Yesu anati kwa iwo, Katsala kanthawi kakang'ono ndipo kuunika kuli mwa inu. 1 Yendani pokhala muli nako kuunika, kuti mdima sungakupezeni; ndipo woyenda mumdima sadziwa kumene amukako,