42 Kungakhale kotero, ambiri a mwa akuru anakhulupirira iye; koma 6 cifukwa ca Afarisi sanabvomereza, kuti angaletsedwe m'sunagoge,
43 7 pakuti anakonda ulemerero wa anthu koposa ulemerero wa Mulungu.
44 Koma Yesu anapfuula nati, 8 iye wokhulupirira ine, sakhulupirira Ine, koma iye wondituma Ine.
45 Ndipo 9 wondiona Ine aona amene anandituma Ine
46 10 Ndadza Ine kuunika ku dziko lapansi, kuti yense wokhulupirira Ine asakhale mumdima.
47 Ndipo ngati wina akumva mau anga, ndi kusawasunga, Ine sindimweruza; pakuti 11 sindinadza kudzaweruza dziko lapansi, koma kuti ndipulumutse dziko lapansi.
48 12 iye amene akaniza Ine, ndi kusalandira mau anga, ali naye womweruza iye; 13 mau amene ndalankhula, iwowa adzamweruza tsiku lomariza.