19 Kuyambira tsopano ndinena kwa inu, cisadacitike, kuti pamene citacitika, mukakhulupire kuti ndine amene.
20 Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Iye wolandira amene ali yense ndimtuma, andilandira Ine; koma wolandira Ine alandira wondituma Ine.
21 Yesu m'mene adanenaizi, anabvutika mumzimu, nacita umboni, nati, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, kuti mmodzi wa inu adzandipereka Ine.
22 Akuphunzira analikupenyanawina kwa mnzace, ndi kusinkhasinkha kuti ananena za yani.
23 Koma mmodzi wa akuphunzira ace, amene Yesu anamkonda, analikutsamira pa cifuwa ca Yesu.
24 Pamenepo Simoni Petro anamkodola nanena naye, Utiuze ndiye yani amene anena za iye.
25 Iyeyu potsamira pomwepo, pa cifuwa ca Yesu, anena ndi iye. Ambuye, ndiye yani?