24 Pamenepo Simoni Petro anamkodola nanena naye, Utiuze ndiye yani amene anena za iye.
25 Iyeyu potsamira pomwepo, pa cifuwa ca Yesu, anena ndi iye. Ambuye, ndiye yani?
26 Ndipo Yesu anayankha, Ndi iyeyu, amene Ine ndidzamsunsira nthongo ndi kumpatsa, Pamenepo, m'mene anasunsa nthongo anaitenga naipatsa Yudase mwana wa Simoni Isikariote.
27 Ndipopambuyo pace pa nthongoyo, Satana analowa mwa iyeyu. Pamenepo Yesu ananena naye, Cimene ucita, cita msanga,
28 Kama palibe mmodzi wa iwo akuseamako anadziwa cimene anafuna, poti atere naye.
29 Pakuti popeza Yudase anali nalo thumba, enaanalikuyesakuti Yesu ananena kwa iye, Gula zimene zitisowa paphwando; kapena, kuti apatse kanthu kwa aumphawi.
30 Pamenepo iyeyo m'mene adalandira nthongo, anaturuka pomwepo, Koma kunali usiku.