15 Ngati mukonda Ine, sungani malamulo anga.
16 Ndipo Ine ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani inu Nkhoswe yina, kuti akhale ndi inu ku nthawi yonse,
17 ndiye Mzimu wa coonadi; amene dziko lapansi silingathe kumlandira, pakuti silimuona iye, kapena kumzindikira iye. Inu mumzindikira iye; cifukwa akhala ndi inu nadzakhala mwa inu.
18 Sindidza-kusiyani inu mukhale ana amasiye; ndidza kwa inu.
19 Katsala kanthawi, ndipo dziko lapansi silindionanso Ine; koma inu mundiona; popeza Ine ndiri ndi moyo inunso mudzakhala ndi moyo.
20 Tsiku lo mwelo mudzazindikira kuti ndiri Ine mwa Atate wanga, ndi inu mwa Ine, ndi Ine mwa inu.
21 Iye wakukhala nao malamulo anga, ndi kuwasunga, iyeyu ndiye wondikonda Ine; koma wondikonda Ine adzakondedwa ndi Atate wanga, ndipo line ndidzamkonda, ndipo ndidzadzionetsandekha kwa iye.