7 Ngati mukhala mwa Ine, ndi mau anga akhala mwa inu, pemphani cimene ciri conse mucifuna ndipo cidzacitika kwa inu.
8 Mwa ici alemekezedwa Atate wanga, kuti mubale cipatso cambiri; ndipo mudzakhala akuphunzira anga.
9 Monga momwe Atate wandikonda Ine, Inenso ndakonda inu; khalani m'cikondi canga.
10 Ngati musunga malamulo anga mudzakhala m'cikondi canga; monga Ine ndasunga malamulo a Atate wanga, ndipo ndikhala m'cikondi cace.
11 Izi ndalankhula ndi inu, kuti cimwemwe canga cikhale mwa inu, ndi kuti cimwemwe canu cidzale.
12 Lamulo langa ndi ili, kuti mukondane wina ndi mnzace, monga ndakonda inu.
13 Palibe munthu ali naco cikondi coposa ici, cakuti munthu ataya moyo wace cifukwa ca abwenzi ace.