14 Iyeyo adzalemekeza Ine; cifukwa adzatenga za mwa Ine, nadzalalikira kwa inu.
15 Zinthu ziri zonse Atate ali nazo ndi zanga; cifukwa cace ndinati, kuti atenga za mwa Ine, nadzalalikira kwa inu.
16 Katsala kanthawi, ndipo simundionanso Ine, ndipo kanthawinso, ndipo mudzandiona Ine.
17 Mwa akuphunzira ace tsono anati wina ndi mnzace, ici nciani cimene anena ndi ife, Kanthawi ndipo simundiona; ndiponso kanthawi, ndipo mudzandiona; ndipo, cifukwa ndimuka kwa Atate?
18 Cifukwa cace ananena, ici nciani cimene anena, Kanthawi? Sitidziwa cimene alankhula.
19 Yesu anazindikira kuti analikufuna kumfunsa iye, ndipo anati kwa iwo, Kodi mulikufunsana wina ndi mnzace za ici, kuti ndinati, Kanthawi ndipo simundiona Ine, ndiponso kanthawi nimudzandiona Ine?
20 Indetu, indetu, ndinena ndi inu, kuti mudzalira ndi kubuma maliro inu, koma dziko lapansi lidzakondwera; mudzacita cisoni inu, koma cisoni canu cidzasandulika cimwemwe.