11 Sindikhalanso m'dziko lapansi, koma iwo ali m'dziko lapansi, ndipo Ine ndidza kwa Inu. Atate. Woyera, sungani awa m'dzina lanu amene mwandipatsa Ine, kuti akhale mmodzi, monga Ife.
12 Pamenendinakhala nao, Ine ndinalikuwasunga iwo m'dzina lanu amene mwandipatsa Ine; ndipo ndinawasunga, ndipo sanatayika mmodzi yense wa iwo, koma mwana wa citayiko, kuti lembo likwaniridwe.
13 Koma tso pane ndidza kwa Inu; ndipo izi ndilankhula m'dziko lapansi, kuti akhale naco cimwemwe canga cokwaniridwa mwa iwo okha.
14 Ine ndawapatsa iwo mau anu; ndipo dziko lapansi linadana nao, cifukwa sakhala a dziko lapansi, monga Ine sindikhala wa dziko lapansi.
15 Sindipempha kuti muwacotse iwo m'dziko lapansi, koma kuti muwasunge iwo kuletsa woipayo.
16 Siali adziko lapansi monga Ine sindiri wa dziko lapansi.
17 Patulani iwo m'coonadi; mau anu ndi coonadi.