3 Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziwe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.
4 Ine ndalemekeza Inu pa dziko lapansi, m'mene ndinatsiriza nchito imene munandipatsa ndicite.
5 Ndipo tsopano, Atate Inu, lemekezani Ine ndi Inu nokha ndi ulemerero umene ndinali nao ndi Inu lisanakhale dziko lapansi.
6 Ndalionetsera dzina lanu kwa anthu amene mwandipatsa Ine m'dziko lapansi; anali anu, ndipo mwandipatsa Ine iwo; ndipo adasunga mau anu.
7 Azindikira tsopane kuti zinthu ziri zonse zimene mwandipatsa Ine zicokera kwa Inu;
8 cifukwa mau amene munandipatsa Ine ndinapatsa iwo; ndipo analandira, nazindikira koona kuti ndinaturuka kwa Inu, ndipo anakhulupira kuti Inu munandituma Ine.
9 Ine ndiwapempherera iwo; sindipempherera dziko lapansi, koma iwo amene mwandipatsa Ine,