1 M'mene Yesu adanena izi, anaturuka ndi akuphunzira ace, kunka tsidya lija la mtsinje wa Kedroni, kumene kunali munda, umene analowamo iye ndi akuphunzira ace.
2 Koma Yudasenso amene akampereka iye, anadziwa malowa; cifukwa Yesu akamkako kawiri kawiri ndi akuphunzira ace.
3 Pamenepo Yudase, m'mene adatenga gulu la asilikari ndi anyamata, kwa ansembe akulu ndi Afarisi, anadza komweko ndi nyali ndi miuni ndi zida.
4 Pamenepo Yesu, podziwa zonse zirinkudza pa iye, anaturuka, nati kwa iwo, Mufuna yani?