7 Ayuda anamyankha iye, Tiri naco cilamulo ife, ndipo monga mwa cilamuloco ayenera kufa, cifukwa anadziyesera Mwana wa Mulungu.
8 Ndipo pamene Pilato anamva mau awa, anaopa koposa.
9 Ndipo analowanso ku Pretorio, nanena kwa Yesu, Mucoka kuti? koma Yesu sanamyankha kanthu.
10 Cifukwa cace Pilato ananena kwa iye, Simulankhula ndi ine kodi? simudziwa kodi kuti ulamuliro ndiri nao wakukumasulani, ndipo ndiri nao ulamuliro wakukupacikani?
11 Yesu anamyankha iye, Simukadakhala nao ulamuliro uli wonse pa Ine, ngati sukadapatsidwa kwa inu kucokera Kumwamba; cifukwa ca ici iye wondipereka Ine kwa inu ali nalo cimo loposa.
12 Pa ici Pilato anafuna kumasula iye; koma Ayuda anapfuula, ndi kunena, Ngati mumasula ameneyo, simuli bwenzi la Kaisara; yense wodziyesera yekha mfumu atsutsana naye Kaisara.
13 Pamenepo Pilato, m'mene adamva mau awa, anaturuka ndi Yesu, nakhala pansi pa mpando woweruzira kumalo dzina lace; Bwalo lamiyala, koma m'Cihebri, Gabata,