4 Yesu nanena naye, Mkazi, ndiri ndi ciani ndi inu? nthawi yanga siinafike.
5 Amace ananena kwa atumiki, Cimene ciri conse akanena kwa inu, citani.
6 Ndipopanali pamenepo mitsuko yamiyala isanu ndi umodzi yoikidwako monga mwa mayeretsedwe a Ayuda, yonse ya miyeso iwiri kapena itatu.
7 Yesu ananena nao, Dzazani mitsukoyo ndi madzi. Naidzaza, nde nde nde.
8 Ndipo ananena nao, Tungani tsopano, mupite nao kwamkulu wa phwando. Ndipo anapita nao.
9 Koma pamene mkuluyo analawa madzi osanduka vinyowo, ndipo sanadziwa kumene anacokera (koma atumiki amene adatiinga madzi anadziwa), mkuluyo anaitana mkwati,
10 nanena naye, Munthu ali yense amayamba kuika vinyo wokoma; ndipo anthu atamwatu, pamenepo wina wosakoma; koma iwe wasunga vinyo wokoma kufikira tsopano lino.